Categories
EKSODO

EKSODO 22

1 Munthu akaba ng’ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng’ombe zisanu pa ng’ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.

2 Akampeza wakuba alimkuboola, nakamkantha kotero kuti wafa, palibe chamwazi.

3 Litamtulukira dzuwa, pali chamwazi; wakubayo azilipa ndithu; ngati alibe kanthu, amgulitse pa umbala wake.

4 Akachipeza chakubacho chili m’dzanja lake chamoyo, ngakhale ng’ombe, kapena bulu, kapena nkhosa, alipe mowirikiza.

5 Munthu akadyetsa choweta pabusa kapena pamunda wampesa, atamasula choweta chake, ndipo chitadya podyetsa pa mwini wake; alipe podyetsa pake poposa, ndi munda wa mphesa wake woposa.

6 Ukayaka moto, nukalandira kuminga, kotero kuti unyeketsa mulu wa tirigu, kapena tirigu wosasenga, kapena munda; woyatsa motoyo alipe ndithu.

7 Munthu akaikiza ndalama kapena chuma kwa mnansi wake, ndipo zibedwa m’nyumba ya munthuyo; akapeza mbala, ilipe chowirikiza.

8 Akapanda kumpeza mbalayo, abwere naye mwini nyumbayo kwa oweruza, kumuyesa ngati anaika dzanja lake pa chuma cha mnansi wake.

9 Mlandu uliwonse wa cholakwa, kunena za ng’ombe, za bulu, za nkhosa, za chovala, za kanthu kalikonse kotayika, munthu anenako kali kake; mlandu wa onse awiri ufike kwa oweruza; iye amene oweruza amtsutsa alipe chowirikiza kwa mnansi wake.

10 Munthu akaikiza bulu, kapena ng’ombe, kapena nkhosa, kapena choweta china kwa mnansi wake, ndipo chikafa, kapena chiphwetekwa, kapena wina achipirikitsa osachiona munthu;

11 lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe.

12 Koma ngati chidabedwa kwaoko ndithu, alipe kwa mwiniyo.

13 Ngati chajiwa ndithu, abwere nacho chikhale mboni; asalipe pa chojiwacho.

14 Munthu akabwereka chinthu kwa mnansi wake, ndipo chiphwetekwa, kapena chifa, mwiniyo palibe, azilipa ndithu.

15 Akakhalapo mwiniyo, asalipe; ngati chagwirira ntchito yakulipira, chadzera kulipira kwake.

Malamulo osiyanasiyana a pakati pa anthu

16 Munthu akanyenga namwali wosapalidwa ubwenzi, nakagona naye, alipetu kuti akhale mkazi wake.

17 Atate wake akakana konse kumpatsa iye, alipe ndalama monga mwa cholipa cha anamwali.

18 Wanyanga usamlola akhale ndi moyo.

19 Aliyense agona ndi choweta aphedwe ndithu.

20 Wakuphera nsembe mulungu wina, wosati Yehova yekha, aonongeke konse.

21 Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m’dziko la Ejipito.

22 Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense.

23 Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;

24 ndi mkwiyo wanga udzayaka, ndipo ndidzapha inu ndi lupanga; ndipo akazi anu adzakhala amasiye, ndi ana anu omwe.

25 Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamuwerengera phindu.

26 Ukati ulandire chikole kaya chovala cha mnansi wako, koma polowa dzuwa uchibwezere kwa iye;

27 popeza chofunda chake ndi ichi chokha, ndicho chovala cha pathupi pake; azifundira chiyani pogona? Ndipo kudzakhala kuti akandifuulira Ine, ndidzamva; pakuti Ine ndine wachisomo.

28 Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.

29 Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.

30 Uzitero nazo ng’ombe zako, ndi nkhosa zako; masiku asanu ndi atatu akhale ndi amai wake; tsiku lachisanu ndi chitatu uzimpereka kwa Ine.

31 Ndipo muzindikhalira Ine anthu opatulika; chifukwa chake musamadya nyama yojiwa kuthengo; itayireni agalu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/22-3fc304c4662b6e5062745e37f8daf452.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *