Categories
EKSODO

EKSODO 25

Zopereka zaufulu zakumanga Malo Opatulika

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Lankhula ndi ana a Israele, kuti anditengere chopereka; ulandire chopereka changa kwa munthu aliyense mtima wake umfunitsa mwini.

3 Ndipo choperekacho uchilandire kwa iwo ndi ichi: golide, ndisiliva, ndi mkuwa,

4 ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ndi ubweya wa mbuzi;

5 ndi zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiira, ndi zikopa za akatumbu, ndi mtengo wakasiya;

6 mafuta akuunikira, zonunkhira za mafuta odzoza, ndi za chofukiza cha fungo lokoma;

7 miyala yaberulo, ndi miyala yoika paefodi, ndi pachapachifuwa.

8 Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao.

9 Monga mwa zonse Ine ndilikuonetsa iwe, chifaniziro cha chihema, ndi chifaniziro cha zipangizo zake zonse, momwemo uchimange.

Za likasa, chotetezerapo, ndi akerubi

10 Ndipo azipanga likasa la mtengo wakasiya: utali wake mikono iwiri ndi hafu, kupingasa kwake mkono ndi hafu, msinkhu wake mkono ndi hafu.

11 Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m’kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.

12 Ndipo uliyengere mphete zinai zagolide, ndi kuziika kumiyendo yake inai; mphete ziwiri pa mbali yake ina, ndi mphete ziwiri pa ina.

13 Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.

14 Nupise mphiko m’mphetezo pa mbali zake za likasa, zakunyamulira nazo likasalo.

15 Mphiko zikhale m’zimphete za likasa; asazisolole.

16 Ndipo uziika m’likasamo mboni imene ndidzakupatsa.

17 Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.

18 Uzipangansoakerubiawiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo.

19 Nupange kerubi mmodzi ku thungo lino, ndi kerubi wina ku thungo lina; upange akerubi ochokera kuchotetezerapo, pa mathungo ake awiri.

20 Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m’mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.

21 Ndipo uziika chotetezerapo pamwamba pa likasa, ndi kuikamo mboni ndidzakupatsayo m’likasamo.

22 Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.

Za gome la mkate woonekera

23 Ndipo uzipanga gome la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri, ndi kupingasa kwake mkono umodzi, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu.

24 Ndipo ulikute ndi golide woona ndi kulipangira mkombero wagolide pozungulira pake.

25 Nulipangire mitanda pozungulirapo yoyesa chikhato m’kupingasa kwake, ndi pamitanda pake pozungulira upangirepo mkombero wagolide.

26 Nulipangire mphete zinai zagolide, ndi kuika mphetezo pangodya zinai zokhala pa miyendo yake inai.

27 Mphetezo zikhale pafupi pa mitanda, zikhale zopisamo mphiko za kunyamulira nazo gome.

28 Ndipo uzipanga mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide, kuti anyamulire nazo gome.

29 Ndipo uzipanga mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo; uzipanga za golide woona.

30 Ndipo uziika mkate woonekera pa gomelo pamaso panga nthawi zonse.

Za choikaponyali

31 Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m’mwemo;

32 ndipo m’mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikaponyalicho zituluke m’mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikaponyalicho zituluke m’mbali inzake.

33 Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi duwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m’choikaponyalicho.

34 Ndipo pa choikaponyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;

35 pakhale mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m’mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m’mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m’choikaponyalicho.

36 Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zotuluka m’mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golide woona.

37 Ndipo uzipanga nyali zake, zisanu ndi ziwiri; ndipo ayatse nyali zake, ziwale pandunji pake.

38 Ndipo mbano zake, ndi zoolera zake, zikhale za golide woona.

39 Achipange ichi ndi zipangizo izi zonse za talente wa golide woona.

40 Ndipo uyang’anire uzipanga monga mwachifaniziro chao, chimene anakuonetsa m’phirimo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/25-3eb74f44fc77334dd16db707f0e1263c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *