Categories
EKSODO

EKSODO 30

Za guwa la nsembe lofukizapo

1 Ndipo upange guwa la nsembe la kufukizapo; ulipange la mtengo wakasiya.

2 Utali wake ukhale mkono, ndi kupingasa kwake mkono; likhale laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zituluke m’mwemo.

3 Ndipo ulikute ndi golide woona, pamwamba pake ndi mbali zake zozungulira, ndi nyanga zake; ulipangirenso mkombero wagolide pozungulira.

4 Ndipo ulipangire mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake; uziike pa nthiti zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri; zikhale zopisamo mphiko kulinyamula nazo.

5 Ndipo upange mphiko za mtengo wakasiya, ndi kuzikuta ndi golide.

6 Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.

7 Ndipo Aroni azifukizapo chofukiza cha zonunkhira zokoma m’mawa ndi m’mawa, pamene akonza nyalizo, achifukize.

8 Ndipo pamene Aroni ayatsa nyalizo madzulo, achifukize chofukiza chosatha pamaso pa Yehova mwa mibadwo yanu.

9 Musafukizapo chofukiza chachilendo, kapena nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa; musathirepo nsembe yothira.

10 Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m’chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.

Ndalama za chiombolo

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

12 Pamene uwerenga ana a Israele, monga mwa mawerengedwe ao, munthu yense apereke kwa Yehova chiombolo cha pa moyo wake, pa kuwerengedwa iwowa; kuti pasakhale mliri pakati pao, pakuwerengedwa iwowa.

13 Ichi achipereke, yense wakupita kwa owerengedwa; limodzi la magawo awiri a sekeli, monga sekeli la malo opatulika; (sekeli ndilo magera makumi awiri,) limodzi la magawo awiri a sekeli, ndilo chopereka cha Yehova.

14 Yense wakupita kwa owerengedwawo, wa zaka makumi awiri ndi wa mphambu zake, apereke choperekacho kwa Yehova.

15 Wachuma asachulukitsepo, ndi osauka asachepse pa limodzi mwa magawo awiri a sekeli, pakupereka chopereka kwa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

16 Ndipo uzilandira ndalama za choteteza kwa ana a Israele, ndi kuzipereka pa ntchito yachihema chokomanako; kuti zikhale chikumbutso cha ana a Israele pamaso pa Yehova, kuchita choteteza cha miyoyo yanu.

Za mkhate wakusambiramo

17 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, ndi kuti,

18 Upangenso mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wakusambiramo; nuuike pakati pa chihema chokomanako ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.

19 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna azisambiramo manja ao ndi mapazi ao;

20 pakulowa iwo m’chihema chokomanako asambe ndi madzi, kuti angafe; kapena poyandikiza guwa la nsembe kutumikirako, kufukiza nsembe yamoto ya Yehova;

21 asambe manja ao ndi mapazi ao, kuti angafe: liwakhalire lemba losatha, kwa iye ndi kwa mbeu zake, mwa mibadwo yao.

Za mafuta odzoza opatulika

22 Yehova ananenanso ndi Mose, ndi kuti,

23 Udzitengerenso zonunkhira zomveka,murewoyenda masekeli mazana asanu ndi sinamoni wonunkhira wa limodzi la magawo awiri a mureyo, ndilo masekeli mazana awiri kudza makumi asanu, ndi nzimbe zonunkhira mazana awiri kudza makumi asanu,

24 ndi kida mazana asanu, monga sekeli la malo opatulika, ndi mafuta a azitona hini limodzi;

25 ndipo ukonze nazo mafuta odzoza opatulika, osakanizika monga mwa machitidwe a wosakaniza; akhale mafuta odzoza opatulika.

26 Ndipo udzoze nao chihema chokomanako, ndi likasa la mboni,

27 ndi guwalo ndi zipangizo zake zonse, ndi choikaponyali ndi zipangizo zake,

28 ndi guwa la nsembe lofukizapo, ndi guwa la nsembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate wosambiramo ndi tsinde lake.

29 Ndipo uzipatule, kuti zikhale zopatulika ndithu; zonse zakuzikhudza zidzakhala zopatulika.

30 Ndipo udzoze Aroni ndi ana ake aamuna, ndi kuwapatula andichitire ntchito ya nsembe.

31 Nulankhule ndi ana a Israele, ndi kuti, Awa ndi mafuta odzoza opatulika a Ine mwa mibadwo yanu.

32 Asawatsanulire pa thupi la munthu; kapena musakonza ena onga awa, mwa makonzedwe ake; awa ndiwo opatulika, muwayese opatulika.

33 Aliyense amene akonza ena otere, kapena aliyense awaika pa mlendo, ameneyo asazidwe kwa anthu a mtundu wake.

Za chofukiza

34 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Udzitengere zonunkhira, natafi, ndi sekeleti, ndi kelebuna; zonunkhira pamodzi ndilubaniloona; miyeso yofanana;

35 ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosakaniza mwa machitidwe a wosakaniza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika;

36 nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m’chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.

37 Koma za chofukizacho uchikonze, musadzikonzere nokha china, mwa makonzedwe ake amene; muchiyese chopatulika cha Yehova.

38 Aliyense wokonza china chotere kununkhizapo, achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/30-c25c7d78d3908644122c0a69ae6bd9de.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *