Categories
EKSODO

EKSODO 32

Fano la mwanawang’ombe

1 Koma pamene anaona kuti Mose anachedwa kutsika m’phiri, anthuwo anasonkhana kwa Aroni, nanena naye, Ukani, tipangireni milungu yakutitsogolera; pakuti Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

2 Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m’makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine.

3 Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m’makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni

4 Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang’ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m’dziko la Ejipito.

5 Pakuchiona Aroni, anamanga guwa la nsembe patsogolo pake; ndipo Aroni anafuula nati, Mawa aliko madyerero a Yehova.

6 Ndipo m’mawa mwake anauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, nabwera nazo nsembe zamtendere; ndi anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nauka kusewera.

7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, tsikatu, pakuti anthu ako udakwera nao kuchokera m’dziko la Ejipito wadziipsa;

8 wapatuka msanga njira imene ndinawauza; wadzinyengera mwanawang’ombe, namgwadira, namphera nsembe, nati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m’dziko la Ejipito.

9 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ndawapenya anthu awa, taona, ndiwo anthu opulupudza;

10 ndipo tsopano ndileke, kuti ndipse mtima pa awo ndi kuwatha, ndi kukuza iwe ukhale mtundu waukulu.

11 Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?

12 Akaneneranji Aejipito, ndi kuti, Anawatulutsa ndi cholinga choipa, kuti awaphe m’mapiri, ndi kuwatha pankhope padziko lapansi? Pepani, lekani choipacho cha pa anthu anu.

13 Kumbukirani Abrahamu, Isaki ndi Israele, atumiki anu, amene munawalumbirira ndi kudzitchula nokha, amene munanena nao, Ndidzachulukitsa mbeu zanu ngati nyenyezi za kuthambo, ndi dziko ili lonse ndanenali ndidzapatsa mbeu zanu, likhale cholowa chao nthawi zonse.

14 Ndipo Yehova analeka choipa adanenachi, kuwachitira anthu ake.

Mose atsikira anthu opembedza fanolo

15 Ndipo Mose anatembenuka, natsika m’phirimo, magome awiri a mboni ali m’dzanja lake; magome olembedwa kwina ndi kwina; analembedwa mbali ina ndi inzake yomwe.

16 Ndipo magomewo ndiwo ntchito ya Mulungu, kulembaku ndiko kulemba kwa Mulungu, kozokoteka pa magomewo.

17 Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono.

18 Koma iye anati, Phokosoli sindilo la kufuula kwa ogonjetsa, kapena la kufuula kwa opasuka; koma phokoso ndikumvali ndilo la othirirana mang’ombe.

19 Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang’ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m’manja mwake, nawaswa m’tsinde mwa phiri.

20 Ndipo anatenga mwanawang’ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele.

21 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?

22 Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba choipa.

23 Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m’dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera.

24 Ndipo ndinanena nao, Aliyense ali naye golide amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m’moto, ndimo anatulukamo mwanawang’ombe uyu.

Alangidwa anthuwo

25 Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao,

26 Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana aamuna onse a Levi anasonkhana kwa iye.

27 Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m’chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake.

28 Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu.

29 Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino.

Mose atetezera anthu kwa Mulungu

30 Ndipo kunali m’mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu.

31 Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide.

32 Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m’buku lanu limene munalembera,

33 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m’buku langa.

34 Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao.

35 Ndipo Yehova anakantha anthu, chifukwa anapanga mwanawang’ombe amene Aroni anapanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/32-0c2c04628693ed7e83ec8132501396db.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *