Mapangidwe a guwa la nsembe yopsereza
1 Ndipo anapanga guwa la nsembe yopsereza la mtengo wakasiya; utali wake mikono isanu, ndi kupingasa kwake mikono isanu, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono itatu.
2 Ndipo anapanga nyanga zake pangodya zake zinai; nyanga zake zinakhala zotuluka m’mwemo; ndipo analikuta ndi mkuwa.
3 Anapanganso zipangizo zonse za guwalo, zotayira, ndi zoolera, ndi mbale zowazira, ndi mitungo, ndi zopalira moto; zipangizo zake zonse anazipanga zamkuwa.
4 Ndipo anapangira guwa la nsembelo sefa, malukidwe ake nja mkuwa, pansi pa khoma lamkati lake wakulekeza pakati pake.
5 Ndipo anayengera mathungo anai a sefa wamkuwayo mphete zinai, zikhale zopisamo mphiko.
6 Napanga mphiko za mtengo wakasiya, nazikuta ndi mkuwa.
7 Ndipo anapisa mphikozo mu mphetezo pa mbali za guwa la nsembe, kulinyamulira nazo; analipanga ndi matabwa, lagweregwere.
Za mkhate wakusambiramo
8 Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo lachihema chokomanako.
Bwalo la chihema
9 Ndipo anapanga bwalo; pa mbali ya kumwera, kumwera, nsalu zotchingira za pabwalo zinali za bafuta wa thonje losansitsa, mikono zana limodzi;
10 nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ao makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva.
11 Ndi pa mbali ya kumpoto mikono zana limodzi, nsichi zake makumi awiri, ndi makamwa ake makumi awiri, amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.
12 Ndi pa mbali ya kumadzulo panali nsalu zotchingira za mikono makumi asanu, nsichi zake khumi, ndi makamwa ake khumi; zokowera za nsichi ndi mitanda yake yasiliva.
13 Ndi pa mbali ya kum’mawa, kum’mawa, mikono makumi asanu.
14 Nsalu zotchingira za pa mbali imodzi ya chipata nza mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu;
15 momwemonso pa mbali ina: pa mbali ino ndi pa mbali ina ya chipata cha pabwalo panali nsalu zotchingira za mikono khumi ndi isanu; nsichi zake zitatu, ndi makamwa ake atatu.
16 Nsalu zotchingira zonse za pabwalo pozungulira zinali za bafuta wa thonje losansitsa.
17 Ndipo makamwa a nsichi anali amkuwa; zokowera za nsichi ndi mitanda yake zasiliva; ndi zokutira mitu yake zasiliva; ndi nsichi zonse za pabwalo zinagwirana pamodzi ndi siliva.
18 Ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo ndiyo ntchito ya wopikula, ya lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; utali wake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake ndi kupingasa kwake mikono isanu, yolingana ndi nsalu zotchingira za pabwalo.
19 Ndi nsichi zake zinali zinai, ndi makamwa ake anai, amkuwa; zokowera zake zasiliva, ndi zokutira mitu yake ndi mitanda yake zasiliva.
20 Ndi zichiri zonse za chihema, ndi za bwalo lake pozungulira, nza mkuwa.
Mawerengo a zopereka za pa chihema
21 Ichi ndi chiwerengo cha zinthu za chihema, chihema cha mboni, monga anaziwerenga, monga mwa mau a Mose, achite nazo Alevi; anaziwerenga Itamara, mwana wa Aroni wansembe.
22 Ndipo Bezalele mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, anapanga zonse zimene Yehova adauza Mose.
23 Ndi pamodzi naye Oholiyabu, mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, ndiye wozokota miyala, ndi mmisiri waluso, ndiponso wopikula ndi lamadzi ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.
24 Golide yense anachita naye mu ntchito yonse ya malo opatulika, golide wa choperekacho, ndicho matalente makumi awiri kudza asanu ndi anai, ndi masekeli mazana asanu ndi awiri, kudza makumi atatu, monga mwa sekeli wa malo opatulika.
25 Ndipo siliva wa iwo owerengedwa a khamulo ndiwo matalente zana limodzi, ndi masekeli chikwi chimodzi, kudza mazana asanu ndi awiri, mphambu makumi asanu ndi awiri kudza asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika.
26 Munthu mmodzi anapereka beka, ndiwo limodzi la magawo awiri la sekeli, kuyesa sekeli wa malo opatulika, anatero onse akupita kunka kwa owerengedwawo, kuyambira munthu wa zaka makumi awiri ndi oposa, ndiwo anthu zikwi mazana asanu ndi limodzi kudza zitatu, ndi mazana asanu mphambu makumi asanu.
27 Ndipo matalente zana limodzi a siliva ndiwo a kuyengera makamwa a malo opatulika, ndi makamwa a nsalu yotchinga; makamwa zana limodzi matalente zana limodzi, talente limodzi kamwa limodzi.
28 Ndipo anapanga zokowera za mizati nsanamira ndi nsichi ndi masekeli aja chikwi chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu asanu, nakuta mitu yake, nazigwirizanitsa pamodzi.
29 Ndi mkuwa wa choperekacho ndiwo matalente makumi asanu ndi awiri, ndi masekeli zikwi ziwiri kudza mazana anai.
30 Ndipo anapanga nao makamwa a pa khomo la chihema chokomanako, ndi guwa la nsembe lamkuwa, ndi sefa wake amkuwa, ndi zipangizo zonse za guwa la nsembe,
31 ndi makamwa a pabwalo pozungulira, ndi makamwa a ku chipata cha pabwalo, ndi zichiri zonse za chihema, ndi zichiri zonse za pabwalo pozungulira.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/38-8143c5d1aa71ad453b45692cb442e49f.mp3?version_id=1068—