Categories
EKSODO

EKSODO 39

Maombedwe a zovala za ansembe

1 Ndipo anaomba zovala zakutumikira nazo ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, atumikire nazo m’malo opatulika, naomba zovala zopatulika za Aroni; monga Yehova adamuuza Mose.

2 Ndipo anaombaefodiwa golide, lamadzi, lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

3 Ndipo anasula golide waphanthiphanthi, nalemba nsambo, kuti amuombe pamodzi ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, ntchito ya m’misiri.

4 Anapangira efodi zapamapewa zolumikizana; pansonga ziwirizo anamlumikiza.

5 Ndi mpango wa efodi wokhala pamenepo, wakummanga nao unali woombera kumodzi wa chiombedwe chomwechi; wa golide, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa; monga Yehova adauza Mose.

6 Ndipo anakonza miyala yasohamu, yogwirika m’zoikamo zagolide, yolocha ngati malochedwe a chosindikizira, ndi maina a ana a Israele.

7 Ndipo anaiika pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya chikumbutso kwa ana a Israele; monga Yehova adamuuza Mose.

Za chapachifuwa

8 Ndipo anaomba chapachifuwa, ntchito ya mmisiri, monga maombedwe ake a efodi; cha golide, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

9 Chinakhala chaphwamphwa; anachiomba chapachifuwa chopindika; utali wake dzanja limodzi, ndi kupingasa kwake dzanja limodzi, chinakhala chopindika.

10 Ndipo anaika pomwepo mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba.

11 Ndi mzere wachiwiri wa nofeki, safiro, ndi yahalomu.

12 Ndi mzere wachitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama.

13 Ndi mzere wachinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; inakhala yogwirika ndi golide maikidwe ake.

14 Ndipo miyalayi inakhala monga mwa maina a ana a Israele, khumi ndi awiri, monga mwa maina ao; ngati malochedwe a chosindikizira, yonse monga mwa maina ake, kwa mafuko khumi ndi awiriwo.

15 Ndipo anapangira pachapachifuwa maunyolo ngati zingwe, ntchito yopota ya golide woona.

16 Anapanganso zoikamo ziwiri zagolide, ndi mphete ziwiri zagolide; naika mphete ziwirizo pansonga ziwiri za chapachifuwa.

17 Ndipo anamanga maunyolo awiri opota agolide pa mphete ziwiri pansonga za chapachifuwa.

18 Ndi nsonga zake ziwiri zina za maunyolo awiri opotawo anazimanga pa zoikamo ziwiri, nazimanga pa zapamapewa za efodi, m’tsogolo mwake.

19 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pansonga ziwiri za chapachifuwa, m’mphepete mwake m’katimo, pa mbali ya kuefodi.

20 Ndipo anapanga mphete ziwiri zagolide, naziika pa zapamapewa ziwiri za efodi pansi pake, pa mbali yake ya kutsogolo, pafupi pa msoko wake, pamwamba pa mpango wa efodi.

21 Ndipo anamanga chapachifuwa pa mphete zake ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti chikhale pa mpango wa efodi, ndi kuti chapachifuwa chisamasuke paefodi; monga Yehova anamuuza Mose.

22 Ndipo anaomba mwinjiro wa efodi, ntchito yoomba ya lamadzi lokha;

23 ndi pakati pake polowa mutu, ngati polowa pa malaya ochingirizira, ndipo anabinyira pozungulira polowa pake, pangang’ambike.

24 Napangira pa mkawo wa mwinjiro makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa.

25 Ndipo anapanga miliu ya golide woona, napakiza miliu ndi makangaza, pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, popakiza ndi makangaza.

26 Mliu ndi khangaza, mliu ndi khangaza pa mkawo wa mwinjiro pozungulira, kutumikira nazo; monga Yehova anamuuza Mose.

27 Ndipo anaomba malaya a bafuta, a ntchito yoomba, a Aroni, ndi a ana ake aamuna,

28 ndi nduwira yabafuta wa thonje losansitsa, ndi akapa okometsetsa a bafuta wa thonje losansitsa, ndi zovala za kumiyendo za bafuta wa thonje losansitsa,

29 ndi mpango wabafuta wa thonje losansitsa, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ntchito ya wopikula; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Ndipo anapanga phanthiphanthi wa korona wopatulika wa golide woona, nalembapo lemba, ngati malochedwe a chosindikizira, KUPATULIKIRA YEHOVA.

31 Namangako mkuzi wamadzi, kuumanga nao pamwamba pa nduwira; monga Yehova adamuuza Mose.

32 Potero anatsiriza ntchito yonse ya Kachisi wachihema chokomanako; ndipo ana a Israele adachita monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, anachita momwemo.

Zopangidwa zonse zionetsedwa kwa Mose

33 Ndipo anabwera naye Kachisi kwa Mose, chihemacho, ndi zipangizo zake zonse, zokowera zake, matabwa ake, mitanda yake, ndi mizati yake, nsanamira zake ndi nsichi zake, ndi makamwa ake;

34 ndi chophimba cha zikopa za nkhosa zamphongo zonyika zofiirira, ndi chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi nsalu yotchinga yotsekera;

35 likasa la mboni, ndi mphiko zake, ndi chotetezerapo;

36 gomelo, zipangizo zake zonse, ndi mkate woonekera;

37 choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;

38 ndi guwa la nsembe lagolide, ndi mafuta odzoza, ndi chofukiza cha fungo lokoma, ndi nsalu yotsekera pa khomo la chihemacho;

39 guwa la nsembe la mkuwa, ndi sefa wake wamkuwa, mphiko zake, ndi zipangizo zake zonse, mkhate ndi tsinde lake;

40 nsalu zotchingira za pabwalo, nsichi zake, ndi makamwa ake, ndi nsalu yotsekera pa chipata cha pabwalo, zingwe zake, ndi zichiri zake, ndi zipangizo zonse za ntchito ya Kachisi, za kuchihema chokomanako;

41 zovala zokoma za kutumikira nazo m’malo opatulika, ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, ndi zovala za ana ake, kuchita nazo ntchito ya nsembe.

42 Monga mwa zonse Yehova adamuuza Mose, momwemo ana a Israele anachita ntchito zonse.

43 Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EXO/39-a24f1625b63445e73f6a173237a20115.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *