Za nsembe yaufa ndi ya zipatso zoyamba
1 Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapolubani.
2 Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake paguwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
3 Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
4 Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta.
5 Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m’chiwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda chotupitsa, wosakaniza ndi mafuta.
6 Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.
7 Ndipo chopereka chako chikakhala nsembe yaufa ya mumphika, chikhale cha ufa wosalala ndi mafuta.
8 Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera nacho kwa wansembe, iyeyo apite nacho ku guwa la nsembe.
9 Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe paguwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.
10 Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
11 Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.
12 Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize paguwa la nsembe zichite fungo lokoma.
13 Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wachipanganocha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.
14 Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kucha, zoumika pamoto, zokonola.
15 Ndipo uthirepo mafuta, ndi kuikapo lubani; ndiyo nsembe yaufa.
16 Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/2-162d45fc8e2fcdd233876d61636b8e6d.mp3?version_id=1068—