Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 7

Chilamulo cha nsembe yopalamula

1 Ndipo chilamulo cha nsembe yopalamula ndi ichi: ndiyo yopatulika kwambiri.

2 Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo aziphera nsembe yopalamula; nawaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

3 Ndipo achotseko, nabwere nao mafuta ake onse; mchira wamafuta, ndi mafuta akukuta matumbo,

4 ndi impso ziwiri, ndi mafuta a pamenepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso;

5 ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe, nsembe yamoto ya kwa Yehova; ndiyo nsembe yopalamula.

6 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; adyere m’malo opatulika; ndiyo yopatulika kwambiri.

7 Monga nsembe yauchimo, momwemo nsembe yopalamula; pa zonse ziwirizi pali chilamulo chimodzi; ikhale yake ya wansembeyo, amene achita nayo chotetezera.

8 Ndipo chikopa cha nsembe yopsereza chikhale chakechake cha wansembe, amene anabwera nayo nsembe yopsereza ya munthu aliyense.

9 Ndipo nsembe zaufa zonse zophika mumchembo, ndi zonse zokonzeka mumphika, ndi pachiwaya, zikhale za wansembe amene wabwera nazo.

10 Ndipo nsembe zonse zaufa zosakaniza ndi mafuta, kapena zouma zikhale za ana onse a Aroni, alandireko onse.

Chilamulo cha nsembe yoyamika

11 Ndipo chilamulo cha nsembe zoyamika, zimene azibwera nazo kwa Yehova ndi ichi:

12 akabwera nayo kuti ikhale nsembe yolemekeza, azibwera nato, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, timitanda topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta, ndi timitanda tootcha, ta ufa wosalala tosakaniza ndi mafuta.

13 Abwere nacho chopereka chake pamodzi ndi timitanda ta mkate wachotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zake.

14 Ndipo pa zopereka zonsezi atengepo ndi kubwera nako kamtanda kamodzi, kuti kakhale ka nsembe yokweza ya kwa Yehova; kakhale ka wansembe wakuwaza mwazi wa nsembe zoyamika.

15 Kunena za nyama ya nsembe yolemekeza ya nsembe zoyamika zake, aziidya tsiku lomwelo lakuipereka; asasiyeko kufikira m’mawa.

16 Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m’mawa adye chotsalirapo;

17 koma chotsalira pa nyama ya nsembeyo tsiku lachitatu, achitenthe.

18 Ndipo akadyako nyama ya nsembe zoyamika zake tsiku lachitatu, sikuvomerezeka kumene; sadzamwerengera wobwera nayo; ndiyo chinthu chonyansa, ndipo munthu wakudyako adzasenza mphulupulu zake.

19 Ndipo nyama yokhudza kanthu kalikonse kodetsa isadyeke; aitenthe ndi moto. Koma za nyama ina, aliyense ayera aidyeko.

20 Koma munthu akadya nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, pokhala nacho chomdetsa, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

21 Ndipo munthu akakhudza chinthu chodetsa, chodetsa cha munthu, kapena chodetsa cha zoweta, kapena chilichonse chonyansa chodetsa, nakadyako nyama ya nsembe zoyamika za Yehova, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Aletsedwa asadye mafuta ndi mwazi

22 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

23 Lankhula ndi ana a Israele ndi kuti, Musamadya mafuta ali onse, a ng’ombe, kapena a nkhosa, kapena a mbuzi.

24 Ndipo mafuta a iyo idafa yokha, ndi mafuta a iyo idajiwa ndi chilombo ayenera ntchito iliyonse, koma musamadya awa konsekonse.

25 Pakuti aliyense akadya mafuta a nyama imene amabwera nayo ikhale nsembe yamoto ya kwa Yehova, munthu amene akadya awa achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

26 Ndipo musamadya mwazi uliwonse, kapena wa mbalame, kapena wa nyama, m’nyumba zanu zonse.

27 Aliyense akadya mwazi uliwonse, munthuyo achotsedwe kwa anthu a mtundu wake.

Za gawo la ansembe

28 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

29 Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Wakubwera nayo nsembe yoyamika yake kwa Yehova, azidza nacho chopereka chake kwa Yehova chochokera ku nsembe yoyamika yake;

30 adze nazo m’manja mwake nsembe zamoto za Yehova; adze nao mafuta pamodzi ndi nganga, kuti aweyule ngangayo ikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

31 Ndipo wansembeyo atenthe mafutawo paguwa la nsembe; koma ngangayo ikhale ya Aroni ndi ana ake.

32 Ndipo mwendo wathako wa ku dzanja lamanja muupereke kwa wansembe ukhale nsembe yokweza yochokera ku nsembe zoyamika zanu.

33 Mwendo wathako wa ku dzanja lamanja ukhale gawo lake la iyeyu mwa ana a Aroni wakubwera nao mwazi wa zopereka zoyamika, ndi mafuta.

34 Pakuti ndatengako kwa ana a Israele, ku nsembe zoyamika zao, nganga ya nsembe yoweyula, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja wa nsembe yokweza; ndipo ndazipereka kwa Aroni wansembe ndi kwa ana ake, zikhale zoyenera iwo kosatha zochokera kwa ana a Israele.

35 Ili ndi gawo la Aroni, ndi gawo la ana ake, lochokera ku nsembe zamoto za Yehova, analinena, tsiku limene Iye anawasendeza alowe utumiki wa ansembe a Yehova;

36 limene Yehova analamula ana a Israele aziwapatsa, tsiku limene Iye anawadzoza. Likhale lemba losatha mwa mibadwo yao.

37 Icho ndi chilamulo cha nsembe yopsereza, cha nsembe yaufa, cha nsembe yauchimo, ndi cha nsembe yopalamula, ndi cha kudzaza dzanja, ndi cha nsembe zoyamika;

38 chimene Yehova analamulira Mose m’phiri la Sinai, tsikuli anauza ana a Israele abwere nazo zopereka zao kwa Yehova, m’chipululu cha Sinai.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/7-81e0e3a7e70e5f00fd75b9a529f818b8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *