Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 8

Kupatulidwa kwa ansembe

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng’ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;

3 nusonkhanitse khamu lonse ku khomo lachihema chokomanako.

4 Ndipo Mose anachita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la chihema chokomanako.

5 Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ichi ndi chimene Yehova adauza kuti chichitike.

6 Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi.

7 Ndipo anamveka ndi malaya a m’kati, nammanga m’chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndiefodi, nammanga m’chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.

8 Ndipo anamuika chapachifuwa; naika m’chapachifuwaUrimu ndi Tumimu.

9 Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

10 Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza chihema, ndi zonse zili m’mwemo, nazipatula.

11 Ndipo anawazako paguwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.

12 Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.

13 Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m’kati, nawamanga m’chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.

14 Ndipo anabwera nayo ng’ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa ng’ombe ya nsembe yauchimo.

15 Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde paguwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.

16 Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha paguwa la nsembe.

17 Koma ng’ombeyo, ndi chikopa chake, ndi nyama yake, ndi chipwidza chake, anazitentha ndi moto kunja kwa chigono; monga Yehova adamuuza Mose.

18 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.

19 Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

20 Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zake; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.

21 Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse paguwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.

Kupatulidwa kwa Aroni ndi ana ake

22 Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa mphongoyo.

23 Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja.

24 Pamenepo anabwera nao ana aamuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo paguwa la nsembe pozungulira.

25 Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

26 ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;

27 anaika zonsezi m’manja mwa Aroni, ndi m’manja mwa ana ake aamuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.

28 Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.

29 Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.

30 Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.

31 Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.

32 Koma chotsalira cha nyama ndi mkate muchitenthe ndi moto.

33 Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.

34 Monga anachita lero lino, momwemo Yehova analamula kuchita, kukuchitirani chotetezera.

35 Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.

36 Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anachita zonse zimene Yehova analamula padzanja la Mose.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/8-a03376c1aa1f275964a32ff735d993af.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *