Categories
NUMERI

NUMERI 2

Malongosoledwe a chigono

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ana a Israele azimanga mahema ao yense ku mbendera yake, ya chizindikiro cha nyumba ya kholo lake; amange mahema ao popenyana ndichihema chokomanakopozungulira.

3 Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m’mawa kotuluka dzuwa ndiwo a mbendera ya chigono cha Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana Yuda ndiye Nasoni mwana wa Aminadabu.

4 Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi.

5 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netanele mwana wa Zuwara.

6 Ndipo khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai.

7 Ndi fuko la Zebuloni: kalonga wa ana a Zebuloni ndiye Eliyabu mwana wa Heloni.

8 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.

9 Owerengedwa onse a chigono cha Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsogolera ulendo.

10 Mbendera ya chigono cha Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri.

11 Ndi khamu lake, ndi olembedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.

12 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiele mwana wa Zurishadai.

13 Ndi khamu lake ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu.

14 Ndi fuko la Gadi; kalonga wa ana a Gadi ndiye Eliyasafu mwana wa Reuwele.

15 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu.

16 Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.

17 Pamenepo khamu la Alevi azimuka nacho chihema chokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pake, monga mwa mbendera zao.

18 Mbendera ya chigono cha Efuremu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efuremu ndiye Elisama mwana wa Amihudi.

19 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu.

20 Ndipo oyandikizana naye ndiwo a fuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliele mwana wa Pedazuri.

21 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri.

22 Ndi fuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidani mwana wa Gideoni.

23 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.

24 Owerengedwa onse a chigono cha Efuremu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lachitatu paulendo.

25 Mbendera ya chigono cha Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezere mwana wa Amisadai.

26 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri.

27 Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a fuko la Asere; ndi kalonga wa ana a Asere ndiye Pagiyele mwana wa Okarani.

28 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi anai mphambu chimodzi kudza mazana asanu.

29 Ndi fuko la Nafutali: ndi kalonga wa ana a Nafutali ndiye Ahira mwana wa Enani.

30 Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.

31 Owerengedwa onse a chigono cha Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi. Iwo ndiwo aziyenda m’mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao.

32 Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israele monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m’zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu.

33 Koma sanawerenge Alevi mwa ana a Israele; monga Yehova adauza Mose.

34 Ndipo ana a Israele anachita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ake, monga mwa nyumba za makolo ake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/2-05704bd6f842bddd0414f7ff95506a7a.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *