Za Balamu ndi Balaki
1 Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, namanga mahema m’zigwa za Mowabu, tsidya la Yordani ku Yeriko.
2 Ndipo Balaki mwana wa Zipori anaona zonse Israele anachitira Aamori.
3 Ndipo Mowabu anachita mantha akulu ndi anthuwo, popeza anachuluka; nada mtima Mowabu chifukwa cha ana a Israele.
4 Ndipo Mowabu anati kwa akulu a Midiyani, Tsopano msonkhano uwu udzanyambita zonse zili pozinga pathu, monga ng’ombe zinyambita msipu wa kubusa. Ndipo Balaki mwana wa Zipori anali mfumu ya Mowabu masiku amenewo.
5 Ndipo anatuma amithenga kwa Balamu mwana wa Beori, ku Petori, wokhala kumtsinje, wa dziko la anthu a mtundu wake, kuti amuitane, ndi kuti, Taonani, anatuluka anthu m’dziko la Ejipito; taonani, aphimba nkhope ya dziko, nakhala popenyana ndi ine.
6 Ndipo tsopano, idzatu, nunditembererere anthu awa; popeza andiposa mphamvu; kapena ndidzawapambana, kuti tiwakanthe, ndi kuti ndiwapirikitse m’dziko; pakuti ndidziwa kuti iye amene umdalitsa adalitsika, ndi iye amene umtemberera atemberereka.
7 Ndipo akulu a Mowabu ndi akulu a Midiyani anamuka ndi mphotho za maula m’dzanja lao; anadza kwa Balamu, nanena naye mau a Balaki.
8 Ndipo ananena nao, Mugone kuno usiku uno, ndidzakubwezerani mau, monga Yehova adzanena ndi ine; pamenepo mafumu a Mowabu anagona ndi Balamu.
9 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?
10 Ndipo Balamu anati kwa Mulungu, Balaki mwana wa Zipori mfumu ya Mowabu, anatumiza kwa ine, ndi kuti,
11 Taonani, anthu awa adatuluka mu Ejipito aphimba nkhope ya dziko, idzatu unditembererere awa; kapena ndidzakhoza kulimbana nao nkhondo, ndi kuwapirikitsa.
12 Koma Mulungu anati kwa Balamu, Usapita nao; usatemberera anthuwa; pakuti adalitsika.
13 Ndipo Balamu anauka m’mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu.
14 Pamenepo akalonga a Mowabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati Alikukana Balamu kudza nafe.
15 Koma Balaki anaonjeza kutumanso akalonga, ochuluka, ndi omveka koposa awa.
16 Ndipo anadza kwa Balamu, nati kwa iye, Atero Balaki mwana wa Zipori, Pasakhaletu chinthu chakukuletsa kudza kwa ine;
17 popeza ndidzakuchitira ulemu waukulu, ndipo zonse unena ndi ine ndidzachita; chifukwa chake idzatu, unditembererere anthu awa.
18 Ndipo Balamu anayankha nati kwa anyamata a Balaki, Chinkana Balaki andipatsa nyumba yake yodzala ndisilivandi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova Mulungu wanga, kuchepsako kapena kuonjezako.
19 Ndikupemphani, tsono, khalani pano inu usiku uno womwe; kuti ndidziwe chomwe Yehova adzanenanso nane.
20 Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu usiku, nanena naye, Akadza kukuitana anthuwa, nyamuka, kunka nao, koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukachite.
21 Pamenepo Balamu anauka m’mawa namanga bulu wake, namuka nao akalonga a ku Mowabu.
22 Koma anapsa mtima Mulungu chifukwa cha kupita iye, ndipo mthenga wa Yehova anadziika m’njira wotsutsana naye. Ndipo anali wokwera pabulu wake, ndi anyamata ake awiri anali naye.
23 Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m’njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m’njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.
24 Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m’njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga.
25 Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.
26 Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.
27 Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo.
28 Ndipo Yehova anatsegula pakamwa pake pa bulu, nati uyu kwa Balamu, Ndakuchitanji, kuti wandipanda katatu tsopano?
29 Pamenepo Balamu anati kwa bulu, Chifukwa wandipeputsa; mukadakhala lupanga m’dzanja langa tsopano, ndikadakupha iwe.
30 Ndipo bulu anati kwa Balamu, Si ndine bulu wako amene umayenda wokwera pa ine chiyambire ndili wako kufikira lero lino? Kodi ndikakuchitira chotere ndi kale lonse? Ndipo anati, Iai.
31 Pamenepo Yehova anapenyetsa maso a Balamu, naona iye mthenga wa Yehova alikuima m’njira, lupanga losolola lili kudzanja, ndipo anawerama mutu wake, nagwa nkhope yake pansi.
32 Ndipo mthenga wa Yehova ananena naye, Wapandiranji bulu wako katatu tsopano? Taona, ndatuluka kuti nditsutsane nawe popeza njira iyi ikugwetsa chamutu pamaso panga;
33 koma bulu anandiona, nandipatukira nthawi izi zitatu pondiona; akadapanda kundipatukira, ndikadakupha iwe ndithu, ndi kumsunga iye wamoyo.
34 Pamenepo Balamu anati kwa mthenga wa Yehova, Ndachimwa, popeza sindinadziwe kuti munaima mondiletsa m’njira; ndipo tsopano, ngati chikuipirani, ndibwerera.
35 Ndipo mthenga wa Yehova anati kwa Balamu, Pita nao anthuwa; koma mau okhaokha ndinena ndi iwe, ndiwo ukanene. Potero Balamu anamuka nao akalonga a Balaki.
36 Pamene Balaki anamva kuti wafika Balamu, anamtulukira kukakomana naye kumzinda wa Mowabu, wokhala m’mphepete mwa Arinoni, ndiwo ku malekezero a malire ake.
37 Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?
38 Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Taonani, ndafika kwa inu; ngati ndili nayo mphamvu konse tsopano kunena kanthu? Mau amene Mulungu aike m’kamwa mwanga ndiwo ndidzanena.
39 Ndipo Balamu anamuka ndi Balaki, nafika iwo ku Kiriyati-Huzoti.
40 Pamenepo Balaki anapha ng’ombe ndi nkhosa, natumizira Balamu, ndi akalonga okhala naye.
41 Ndipo kunali kuti m’mawa, Balaki anatenga Balamu, nakwera naye ku misanje yaBaala, ndi kumeneko anaona malekezero a anthuwo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/22-94f83caa4e965d0c823e45d0c7cbd79b.mp3?version_id=1068—