Aisraele achita chigololo napembedza mafano ku Sitimu
1 Ndipo Israele anakhala mu Sitimu, ndipo anthu anayamba kuchita chigololo ndi ana aakazi a Mowabu;
2 popeza anaitana anthuwo adze ku nsembe za milungu yao; ndipo anthuwo anadya, nagwadira milungu yao.
3 Pamene Israele anaphatikana ndi Baala-Peori, Yehova anapsa mtima pa Israele.
4 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Gwira akulu onse a anthu nuwapachikire Yehova, pali dzuwa poyera, kuti mkwiyo waukali wa Yehova uchoke kwa Israele.
5 Ndipo Mose anati kwa oweruza a Israele, Iphani, yense anthu ake adaphatikanawo ndi Baala-Peori.
6 Ndipo, taonani, anadza wina wa ana a Israele, nabwera naye mkazi Mmidiyani kudza naye kwa abale ake, pamaso pa Mose, ndi pamaso pa khamu lonse la ana a Israele, pakulira iwo pa khomo lachihema chokomanako.
7 Pamene Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, anachiona, anauka pakati pa khamu, natenga nthungo m’dzanja lake;
8 natsata munthu Mwisraele m’hema, nawapyoza onse awiri, munthu Mwisraele ndi mkaziyo m’mimba mwake. Pamenepo mliri unaletseka kwa ana a Israele.
9 Ndipo akufa nao mliri ndiwo zikwi makumi awiri ndi zinai.
10 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
11 Finehasi mwana wa Eleazara, mwana wa Aroni wansembe, wabweza kuzaza kwanga pa ana a Israele, popeza anachita nsanje ndi nsanje yanga pakati pao, kotero kuti sindinawathe ana a Israele m’nsanje yanga.
12 Chifukwa chake nena, Taonani, ndimpatsa iye pangano langa la mtendere;
13 ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.
14 Koma dzina la Mwisraele adamuphayo, ndiye amene adamupha pamodzi ndi mkazi Mmidiyani, ndiye Zimiri mwana wa Salu, mfumu ya nyumba ya makolo mwa Asimeoni.
15 Ndi dzina la mkazi Mmidiyani adamuphayo ndiye Kozibi mwana wamkazi wa Zuri; ndiye mkulu wa anthu a nyumba ya makolo mu Midiyani.
16 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17 Sautsa Amidiyani ndi kuwakantha;
18 popeza akusautsani ndi manyengo ao amene anakunyengani nao; m’chija cha Peori, ndi cha Kozibi, mwana wamkazi wa kalonga wa ku Midiyani, mlongo wao, amene adamupha tsiku la mliri, m’chija cha Peori.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NUM/25-2268008534910ad26d12eecead70269e.mp3?version_id=1068—