Achenjere nao owanyenga kuwapembedzetsa mafano
1 Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto, nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa;
2 ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu ina, imene simunaidziwe, ndi kuitumikira;
3 musamamvera mau a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu; popeza Yehova Mulungu wanu akuyesani, kuti adziwe ngati mukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
4 Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.
5 Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, nakuombolani m’nyumba ya ukapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.
6 Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m’tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;
7 ndiyo milungu ya mitundu ya anthu akuzungulira inu, akukhala pafupi pali inu, kapena akukhala patali pali inu, kuyambira malekezero a dziko lapansi kufikira malekezero ena a dziko lapansi;
8 musamavomerezana naye, kapena kumvera iye; diso lanu lisamchitire chifundo, kapena kumleka, kapena kumbisa;
9 koma muzimupha ndithu; liyambe dzanja lanu kukhala pa iye kumupha, ndi pamenepo dzanja la anthu onse.
10 Nimuzimponya miyala, kuti afe; popeza anayesa kukuchetani muleke Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m’dziko la Ejipito, m’nyumba ya ukapolo.
11 Kuti Israele yense amve, ndi kuopa, ndi kusaonjeza kuchita choipa chotere chonga ichi pakati pa inu.
12 Ukamva za umodzi wa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani kukhalako, ndi kuti,
13 Amuna ena opanda pake anatuluka pakati pa inu, nacheta okhala m’mzinda mwao, ndi kuti, Timuke titumikire milungu ina, imene simunaidziwe;
14 pamenepo muzifunsira, ndi kulondola, ndi kufunsitsa; ndipo taonani, chikakhala choona, chatsimikizika chinthuchi, kuti chonyansa chotere chachitika pakati pa inu;
15 muzikanthatu okhala m’mzinda muja ndi lupanga lakuthwa; ndi kuononga konse, ndi zonse zili m’mwemo, ng’ombe zake zomwe, ndi lupanga lakuthwa.
16 Ndipo muzikundika zofunkha zake zonse pakati pakhwalala pake, nimutenthe ndi moto mzinda, ndi zofunkha zake zonse konse, pamaso pa Yehova Mulungu wanu; ndipo udzakhala mulu ku nthawi zonse; asaumangenso.
17 Ndipo pasamamatire padzanja panu kanthu ka chinthu choti chionongeke; kuti Yehova aleke mkwiyo wake waukali, nakuchitireni chifundo, ndi kukumverani nsoni, ndi kukuchulukitsani monga analumbirira makolo anu;
18 pakumvera inu mau a Yehova Mulungu wanu, kusunga malamulo ake onse amene ndikuuzani lero lino, kuchita zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/13-6ddffa2d6d727e49c0b84354adcf0191.mp3?version_id=1068—