Categories
DEUTERONOMO

DEUTERONOMO 18

Zoyenera ansembe ndi Alevi

1 Ansembe Alevi, fuko lonse la Levi, alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi Israele; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi cholowa chake.

2 Alibe cholowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wake ndiye cholowa chao, monga ananena nao.

3 Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng’ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m’masaya ndi chifu.

4 Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.

5 Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mafuko anu onse, aimirire natumikire m’dzina la Yehova, iwo ndi ana ao aamuna kosalekeza.

6 Ndipo Mlevi akachokera kumudzi wanu wina mu Israele monse, kumene akhalako, nakadza ndi chifuniro chonse cha moyo wake ku malo amene Yehova adzasankha;

7 pamenepo azitumikira m’dzina la Yehova Mulungu wake, monga amachita abale ake onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.

8 Chakudya chao chizifanana, osawerengapo zolowa zake zogulitsa.

Mulungu aipidwa nao anyanga ndi obwebweta ndi onse otere

9 Mutakalowa m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa zaamitunduaja.

10 Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.

11 Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.

12 Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.

13 Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.

14 Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kuchita chotero.

Lonjezo lakuti adzabadwa mneneri womveka

15 Yehova Mulungu wanu adzakuukitsiranimneneriwa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;

16 monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu mu Horebu, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso moto waukulu uwu, kuti tingafe.

17 Ndipo Yehova anati kwa ine, Chokoma ananenachi.

18 Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m’kamwa mwake, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.

19 Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m’dzina langa, ndidzamfunsa.

20 Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m’dzina langa, amene sindinamlamulire anene, kapena kunena m’dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe.

21 Ndipo mukati m’mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene?

22 Mneneri akanena m’dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/DEU/18-acddb736ae7b1b77e4e4487a2c5bafbf.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *