1 Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;
2 ndipo yendani m’chikondi mongansoKhristuanakukondani inu, nadzipereka yekha m’malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
3 Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;
4 kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.
5 Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
6 Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
7 Chifukwa chake musakhale olandirana nao;
8 pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,
9 pakuti chipatso cha kuunika tichipeza mu ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi,
10 kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani;
11 ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;
12 pakuti zochitidwa nao m’tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.
13 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika.
14 Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.
15 Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;
16 akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
17 Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani.
18 Ndipo musaledzere naye vinyo, m’mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu,
19 ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m’malimba Ambuye mumtima mwanu;
20 ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu;
21 ndi kumverana wina ndi mnzake m’kuopa Khristu.
Zoyenera m’banja la munthu
22 Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.
23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.
24 Komatu monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m’zinthu zonse.
25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m’malo mwake;
26 kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;
27 kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema.
28 Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;
29 pakuti munthu sanadane nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo;
30 pakuti tili ziwalo za thupi lake.
31 Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.
32 Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo.
33 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EPH/5-43f656087d7fb0dd053cc1e9587b607d.mp3?version_id=1068—