Categories
YOSWA

YOSWA 4

Aimiritsa miyala 12 ikhale chikumbutso ku Giligala

1 Ndipo kunali, utatha kuoloka Yordani mtundu wonse, Yehova ananena ndi Yoswa, nati,

2 Mudzitengere mwa anthu, amuna khumi ndi awiri, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

3 ndipo muwalamulire iwo ndi kuti, Mudzitengere pano pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe, miyala khumi ndi iwiri, ndi kuoloka nayo, ndi kuiika m’mogona m’mene mugonamo usiku uno.

4 Pamenepo Yoswa anaitana amuna khumi ndi awiriwo amene anawaikiratu mwa ana a Israele, fuko limodzi mwamuna mmodzi;

5 nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;

6 kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m’tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?

7 Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo palikasa la chipanganocha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.

8 Ndipo ana a Israele anachita monga Yoswa anawalamulira, nasenza miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, monga Yehova adalankhula ndi Yoswa, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele; ndipo anaoloka nayo kunka kogona, naiika komweko.

9 Ndipo Yoswa anaimika miyala khumi ndi iwiri pakati pa Yordani, poimapo mapazi a ansembe akusenza likasa la chipangano; ikhala komweko kufikira lero lino.

10 Pakuti ansembe akusenza likasa anaima pakati pa Yordani, mpaka zitatha zonse Yehova adazilamulira Yoswa anene kwa anthu, monga mwa zonse Mose adalamulira Yoswa; ndipo anthu anafulumira kuoloka.

11 Ndipo kunali, atatha kuoloka anthu onse, likasa la Yehova linaoloka, ndi ansembe, pamaso pa anthu.

12 Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase anaoloka ndi zida zao pamaso pa ana a Israele, monga Mose adanena nao;

13 ngati zikwi makumi anai ankhondo okonzeka anaoloka pamaso pa Yehova kuthira nkhondo ku zidikha za Yeriko.

14 Tsiku lomwelo Yehova anakulitsa Yoswa pamaso pa Aisraele onse; ndipo anamuopa monga anaopa Mose, masiku onse a moyo wake.

15 Ndipo Yehova anati kwa Yoswa,

16 Lamulira ansembe akusenza likasa la umboni, kuti akwere kutuluka mu Yordani.

17 Pamenepo Yoswa analamulira ansembe, ndi kuti, Kwerani kutuluka mu Yordani.

18 Ndipo kunali, atakwera ansembe akusenza likasa la chipangano la Yehova, kutuluka pakati pa Yordani, nakwera pamtunda mapazi a ansembe, madzi a mu Yordani anabwera m’njira mwake, nasefuka m’magombe ake onse monga kale.

19 Ndipo anthu anakwera kutuluka mu Yordani tsiku lakhumi la mwezi woyamba, namanga misasa ku Giligala, mbali ya ku m’mawa kwa Yeriko.

20 Ndipo Yoswa anaimika ku Giligala miyala ija khumi ndi iwiri adaitenga mu Yordani.

21 Ndipo anati kwa ana a Israele, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani?

22 Pamenepo muzidziwitsa ana anu, ndi kuti, Israele anaoloka Yordani uyu pouma.

23 Pakuti Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yordani pamaso panu, mpaka mutaoloka; monga Yehova Mulungu wanu anachitira Nyanja Yofiira, imene anaiphwetsa pamaso pathu, mpaka titaoloka;

24 kuti mitundu yonse ya padziko lapansi idziwe dzanja la Yehova, kuti ndilo lamphamvu; kuti iope Yehova Mulungu wanu masiku onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/4-f438774cf7afbf99465fb9017ed25607.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *