Kupasulidwa kwa Yeriko
1 Koma ku Yeriko anatseka pazipata, natsekedwa chifukwa cha ana a Israele, panalibe wotuluka, panalibenso wolowa.
2 Ndipo Yehova ananena kwa Yoswa, Taona, ndapereka m’dzanja lako Yeriko ndi mfumu yake, ndi ngwazi zake.
3 Ndipo muzizungulira mzinda inu nonse ankhondo, kuuzungulira mzinda kamodzi. Muzitero masiku asanu ndi limodzi.
4 Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.
5 Ndipo kudzakhala kuti akaliza chilizire ndi nyanga ya nkhosa yamphongo, nimumva kulira kwa mphalasa, anthu onse afuule mfuu yaikulu; ndipo linga la mzindawo lidzagwa pomwepo, ndi anthu adzakwera ndi kulowamo yense kumaso kwake.
6 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzanilikasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.
7 Nati kwa anthu, Pitani, muzizungulira mzinda, ndi ankhondo ndi zida zao atsogolere likasa la Yehova.
8 Ndipo atanena kwa anthu Yoswa, ansembe asanu ndi awiri akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo pamaso pa Yehova, anapita naliza mphalasazo; ndipo likasa la chipangano cha Yehova linawatsata.
9 Ndipo okonzeka kunkhondo anatsogolera ansembe akuliza mphalasa, koma akudza m’mbuyo anatsata likasa, ansembe ali chiombere poyenda iwo.
10 Ndipo Yoswa analamulira anthu, ndi kuti, Musamafuula, kapena kumveketsa mau anu, asatuluke konse mau m’kamwa mwanu, mpaka tsiku lakunena nanu ine, Fuulani; pamenepo muzifuula.
11 Ndipo anazungulitsa likasa la Yehova mzinda, kuzungulira kamodzi; pamenepo analowa kuchigono, nagona m’mwemo.
12 Ndipo Yoswa analawira mamawa, ndi ansembe anasenza likasa la Yehova.
13 Ndipo ansembe asanu ndi awiri, akunyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo ndi kutsogolera nazo likasa la Yehova, anayenda chiyendere naliza mphalasazo; ndi okonzeka kunkhondowo anawatsogolera, ndi akudza m’mbuyo anatsata likasa la Yehova, ansembe ali chiombere poyenda iwo.
14 Ndipo tsiku lachiwiri anazungulira mzinda kamodzi, nabwera kuchigono; anatero masiku asanu ndi limodzi.
15 Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri analawira mamawa, mbandakucha, nazungulira mzinda mommuja kasanu ndi kawiri; koma tsiku lijalo anazungulira mzinda kasanu ndi kawiri.
16 Ndipo kunali, pa nthawi yachisanu ndi chiwiri, pamene ansembe analiza mphalasa, Yoswa anati kwa anthu, Fuulani; pakuti Yehova wakupatsani mzindawo.
17 Koma mzindawo udzaperekedwa kwa Yehova ndi kuonongeka konse, uwu ndi zonse zili m’mwemo; Rahabi yekha wadamayo adzakhala ndi moyo, iye ndi onse ali naye m’nyumba, chifukwa anabisa mithenga tinawatumawo.
18 Ndipo inu, musakhudze choperekedwacho, mungadziononge konse, potapa choperekedwacho; ndi kuononga konse chigono cha Israele ndi kuchisautsa.
19 Komasilivayense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m’mosungira chuma cha Yehova.
20 Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m’mzinda, yense kumaso kwake; nalanda mzindawo.
Apulumutsidwa Rahabi
21 Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m’mzinda, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng’ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa.
22 Ndipo Yoswa ananena kwa amuna awiri anazonda dzikowo, Lowani m’nyumba ya mkazi wadamayo, ndi kutulutsamo mkaziyo ndi zonse ali nazo, monga munamlumbirira iye.
23 Pamenepo anyamata ozondawo analowa, natulutsa Rahabi, ndi atate wake ndi mai wake ndi abale ake, ndi onse anali nao; anatulutsanso achibale ake onse; nawaika kunja kwa chigono cha Israele.
24 Ndipo anatentha mzinda ndi moto, ndi zonse zinali m’mwemo; koma siliva ndi golide ndi zotengera zamkuwa ndi zachitsulo anaziika m’mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.
25 Koma Rahabi, mkazi wadamayo ndi banja la atate wake, ndi onse anali nao, Yoswa anawasunga ndi moyo; ndipo anakhala pakati pa Israele mpaka lero lino; chifukwa anabisa mithenga imene Yoswa anaituma kuzonda Yeriko.
26 Ndipo Yoswa anawalumbirira nyengo ija, ndi kuti, Wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzauka ndi kumanga mzinda uwu wa Yeriko; adzamanga maziko ake ndi kutayapo mwana wake woyamba, nadzaimika zitseko zake ndi kutayapo mwana wake wotsirizira.
27 Potero Yehova anakhala ndi Yoswa; ndi mbiri yake inabuka m’dziko lonse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/6-377a297cb3168c6f4e263aaf50c6f9da.mp3?version_id=1068—