Categories
YOSWA

YOSWA 13

Chigawo cha dziko la kum’mawa kwa Yordani

1 Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikulukulu, alilandire cholowa chao.

2 Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,

3 kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;

4 kumwera dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeki, mpaka ku malire a Aamori;

5 ndi dziko la Agebala, ndi Lebanoni, lonse kum’mawa, kuyambira Baala-Gadi pa tsinde la phiri la Heremoni, mpaka polowera pake pa Hamati;

6 nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebanoni, mpaka Misirefoti-Maimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israele, koma limeneli uwagawire Aisraele, likhale cholowa chao, monga ndinakulamulira.

7 Ndipo tsopano uwagawire mafuko asanu ndi anai, ndi hafu la fuko la Manase, dziko ili likhale cholowa chao.

8 Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira cholowa chao, chimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordani kum’mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

9 kuyambira pa Aroere, wokhala m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa, ndi chidikha chonse cha Medeba mpaka ku Diboni;

10 ndi mizinda yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakuchita ufumu mu Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni;

11 ndi Giliyadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Heremoni, ndi Basani lonse mpaka ku Saleka;

12 ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.

13 Koma ana a Israele sanainge Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israele, mpaka lero lino.

14 Koma fuko la Levi sanalipatse cholowa; nsembe za Yehova Mulungu wa Israele, zochitika ndi moto, ndizo cholowa chake, monga Iye adanena naye.

15 Ndipo Mose anapatsira fuko la ana a Rubeni monga mwa mabanja ao.

16 Malire ao anayambira ku Aroere wokhala m’mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi mzinda uli pakati pa chigwa ndi chidikha chonse cha ku Medeba;

17 Hesiboni ndi mizinda yake yonse yokhala pachidikha; Diboni, ndi Bamoti-Baala ndi Bete-Baala-Meoni;

18 ndi Yahazi ndi Kedemoti, ndi Mefaati;

19 ndi Kiriyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m’phiri la kuchigwa;

20 ndi Betepeori, ndi matsikiro a Pisiga, ndi Beteyesimoti;

21 ndi mizinda yonse ya kuchidikha, ndi ufumu wonse wa Sihoni mfumu ya Aamori, wochita ufumu mu Hesiboni, amene Mose anamkantha pamodzi ndi akalonga a Midiyani, Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri ndi Reba, akalonga a Sihoni, nzika za m’dziko.

22 Ana a Israele anaphanso ndi lupanga Balamu mwana wa Beori, mlauli uja, pamodzi ndi ena adawaphawo.

23 Ndipo malire a ana a Rubeni ndiwo Yordani ndi malire ake. Ndicho cholowa cha ana a Rubeni monga mwa mabanja ao, mizinda yake ndi midzi yake.

24 Ndipo Mose anapatsira fuko la Gadi, ana a Gadi, monga mwa mabanja ao.

25 Ndipo malire ao ndiwo Yazere, ndi mizinda yonse ya Giliyadi, ndi dziko la ana a Amoni logawika pakati, mpaka ku Aroere, wokhala chakuno cha Raba;

26 ndi kuyambira Hesiboni mpaka Ramati-Mizipe, ndi Betonimu; ndi kuyambira Mahanaimu mpaka malire a Debiri;

27 ndipo m’chigwa Beteharamu, ndi Betenimura, ndi Sukoti, ndi Zafoni, chotsala cha ufumu wa Sihoni mfumu ya Hesiboni, Yordani ndi malire ake, mpaka malekezero a nyanja ya Kinereti, tsidya lija la Yordani kum’mawa.

28 Ichi ndi cholowa cha ana a Gadi, monga mwa mabanja ao, mizinda yake ndi midzi yake.

29 Mose anaperekanso cholowa kwa hafu la fuko la Manase, ndicho cha hafu la fuko la Manase monga mwa mabanja ao.

30 Ndipo malire ao anayambira ku Mahanaimu, Basani lonse, ufumu wonse wa Ogi mfumu ya ku Basani, ndi mizinda yonse ya Yairi, yokhala mu Basani, mizinda makumi asanu ndi limodzi;

31 ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.

32 Izi ndi zolowazi Mose anazigawira m’zidikha za Mowabu, tsidya ilo la Yordani ku Yeriko, kum’mawa.

33 Koma fuko la Levi, Mose analibe kulipatsa cholowa: Yehova Mulungu wa Israele, ndiye cholowa chao, monga ananena nao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOS/13-18dc620e1811bebd2b1c80fd8da78e82.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *