Mngelo wa Mulungu adzudzula Aisraele
1 Ndipo mthenga wa Yehova anakwera kuchokera ku Giligala kunka ku Bokimu. Ndipo anati, Ndinakukweretsani kuchokera ku Ejipito, ndi kulowetsa inu m’dziko limene ndinalumbirira makolo anu; ndipo ndinati, Sindidzathyolachipanganochanga nanu ku nthawi yonse;
2 ndipo inu, musamachita pangano ndi nzika za m’dziko ili; muzigamula maguwa ao a nsembe. Koma simunamvere mau anga; mwachichita ichi chifukwa ninji?
3 Chifukwa chakenso ndinati, Sindidzawapirikitsa kuwachotsa pamaso panu; koma adzakhala ngati minga m’nthiti zanu, ndi milungu yao idzakhalira inu msampha.
4 Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.
5 Potero analitcha dzina la malowo Bokimu: namphera Yehova nsembe pomwepo.
Aisraele alowerera atamwalira Yoswa
6 Pamene Yoswa atawalola anthu amuke, ana a Israele anamuka, yense ku cholowa chake, dziko likhale laolao.
7 Ndipo anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a Yoswa, ndi masiku onse a akuluakulu otsala atafa Yoswa, amene adaona ntchito yaikulu yonse ya Yehova anaichitira Israele.
8 Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova anafa wa zaka zake zana ndi khumi.
9 Ndipo anamuika m’malire a cholowa chake mu Timnati-Heresi, ku mapiri a Efuremu, kumpoto kwa phiri la Gaasi.
10 Ndiponso mbadwo uwu wonse unasonkhanidwa kuikidwa kwa makolo ao; nuuka mbadwo wina pambuyo pao; wosadziwa Yehova kapena ntchitoyi adaichitira Israele.
11 Ndipo ana a Israele anachita choipa pamaso pa Yehova, natumikira Abaala;
12 nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m’dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.
13 Ndipo anasiya Yehova, natumikira Baala ndiAsitaroti.
14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele, ndipo anawapereka m’manja a ofunkha kuti awafunkhe; nawagulitsa m’dzanja la adani ao akuwazungulira osakhozanso iwowo kuima pamaso pa adani ao.
15 Kuli konse anatuluka, dzanja la Yehova linawakhalira moipa, monga Yehova adanena, ndi monga Yehova adawalumbirira; nasautsika kwambiri iwowa.
16 Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m’dzanja la iwo akuwafunkha.
17 Koma sanamvere angakhale oweruza ao, pakuti anamuka kupembedza milungu ina, naigwadira; anapatuka msanga m’njira yoyendamo makolo ao, pomvera malamulo a Yehova; sanatero iwowa.
18 Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m’dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.
19 Koma kunali atafa woweruzayo anabwerera m’mbuyo, naposa makolo ao ndi kuchita moipitsa, ndi kutsata milungu ina kuitumikira ndi kuigwadira, sanaleke kanthu ka machitidwe ao kapena ka njira yao yatcheni.
20 Ndipo mkwiyo wa Yehova unayakira Israele; nati Iye, Popeza mtundu uwu unalakwira chipangano changa chimene ndinalamulira makolo ao, osamvera mau anga;
21 Inenso sindionjeza kuingitsa pamaso pao a mitundu ina imene Yoswa adaisiya pakufa iyeyu;
22 kuti ndiyese nayo Israele ngati adzasunga njira ya Yehova kuyendamo monga anaisunga makolo ao, kapena iai.
23 Motero Yehova analeka mitundu iyi osaiingitsa msanga, ndipo sadaipereke m’dzanja la Yoswa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/2-2505c2e715f0948e077fe96f11a42d82.mp3?version_id=1068—