Categories
OWERUZA

OWERUZA 7

Gideoni apirikitsa nkhondo ya Amidiyani

1 Pamenepo Yerubaala, ndiye Gideoni, ndi anthu onse okhala naye anauka mamawa, namanga misasa pa chitsime cha Harodi, ndi misasa ya Midiyani inali kumpoto kwao, paphiri la More m’chigwa.

2 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni. Anthu ali ndi iwe andichulukira kuti ndipereke Midiyani m’dzanja lao; angadzitame Israele pa Ine, ndi kuti, Dzanja la ine mwini landipulumutsa.

3 Ndipo tsopano, kalalike m’makutu a anthu, ndi kuti, Aliyense wochita mantha, nanjenjemera, abwerere nachoke paphiri la Giliyadi. Ndipo anabwererako anthu zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, natsalako zikwi khumi.

4 Ndipo Yehova ananena ndi Gideoni, Anthu akali ochuluka; tsikira nao kumadzi, ndipo ndidzakuyesera iwo komweko; ndipo kudzali kuti iye amene ndimnena kwa iwe, Uyo azimuka nawe, yemweyo azimuka nawe; koma aliyense ndimnena kwa iwe, Uyo asamuke nawe, yemweyo asamuke.

5 Ndipo anatsikira nao anthu kumadzi; ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Aliyense akapiza madzi pa lilime lake, monga akhatira galu, ameneyo amuike pa yekha; momwemo aliyense agwada pakumwa.

6 Ndi kuwerenga kwa iwo akukhatira, ndi kuika dzanja lao kukamwa kwao, ndiko mazana atatu; koma ena onse anagwada pakumwa madzi.

7 Ndipo Yehova anati kwa Gideoni, Ndi anthu mazana atatu akukhatira ndidzakupulumutsani, ndi kupereka Amidiyani m’dzanja lako; koma amuke anthu awa onse, yense kumalo kwake.

8 Pamenepo anthu anatenga kamba m’dzanja lao, ndi malipenga ao; ndipo anauza amuna onse a Israele amuke, yense kuhema kwake; koma anaimika amuna mazana atatuwo; ndipo misasa ya Midiyani inali kunsi kwake m’chigwa.

9 Ndipo kunali usiku womwewo, kuti Yehova ananena naye, Tauka, tatsikira kumisasa; pakuti ndaipereka m’dzanja lako.

10 Koma ngati uopa kutsika, utsike naye Pura mnyamata wako kumisasa;

11 nudzamva zonena iwo; utatero manja ako adzalimbikitsidwa kutsikira kumisasa. Pamenepo anatsikira ndi Pura mnyamata wake ku chilekezero cha anthu azida a m’misasa.

12 Ndipo Amidiyani ndi Aamaleke ndi ana onse a kum’mawa ali gonere m’chigwa, kuchuluka kwao ngati dzombe; ndingamirazao zosawerengeka, kuchuluka kwao ngati mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.

13 Ndipo pakufikako Gideoni, taonani, panali munthu analikufotokozera mnzake loto, nati, Taona, kulota ndinalota, ndipo tapenya, mtanda wa mkate wabarele unakunkhulirakunkhulira m’misasa ya Midiyani, nufika kuhema, numgunda nagwa, numpidigula kuti hema anakhala chigwere.

14 Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m’misasa onse m’dzanja lake.

15 Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m’misasa a Midiyani m’dzanja lanu.

16 Ndipo anagawa amuna mazana atatu akhale magulu atatu, napatsa malipenga m’manja a iwo onse, ndi mbiya zopanda kanthu, ndi miuni m’kati mwa mbiyazo.

17 Ndipo ananena nao, Mundipenyerere ine, ndi kuchita momwemo; ndipo taonani, pakufika ine pa chilekezero cha misasa, kudzali, monga ndichita ine, momwemo muzichita inu.

18 Pamene ndiomba lipenga, ine ndi onse okhala nane, inunso muziomba lipenga pozungulira ponse pa misasa, ndi kunena kuti, Yehova ndi Gideoni.

19 Motero Gideoni ndi amuna zana anali naye anafikira ku chilekezero cha misasa poyambira ulonda wa pakati, atasintha alonda tsopano apa; ndipo anaomba malipenga, naphwanya mbiya zokhala m’manja mwao.

20 Ndi magulu atatuwo anaomba malipenga, naswa mbiyazo, nagwira miuni ndi dzanja lao lamanzere, ndi malipenga m’dzanja lao lamanja kuwaomba; ndipo anafuula, Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.

21 Ndipo anaima yense m’mbuto mwake pozungulira misasa; pamenepo anathamanga a m’misasa onse, nafuula, nathawa.

22 Ndipo mazana atatuwa anaomba malipenga, ndipo Yehova anakanthanitsa yense mnzake ndi lupanga m’misasa monse; ndi a m’misasa anathawa mpaka ku Betesita ku Zerera, mpaka ku malire a Abele-Mehola pa Tabati.

23 Pamenepo anthu a Israele analalikidwa kuchokera ku Nafutali, ndi ku Asere, ndi ku Manase yense, nalondola Amidiyani.

24 Gideoni anatumanso mithenga ku mapiri onse a Efuremu ndi kuti, Tsikani, kukomana ndi Amidiyani ndi kutsekereza madooko asanafike iwowa, mpaka ku Betebara ndi Yordani. Potero amuna onse a Efuremu anasonkhana pamodzi natsekereza madooko mpaka ku Betebara, ndi Yordani.

25 Ndipo anagwira akalonga awiri a Midiyani, Orebu ndi Zeebu; namupha Orebu ku thanthwe la Orebu; ndi Zeebu anamupha ku choponderamo mphesa cha Zeebu, nalondola Amidiyani; ndipo anadza nayo mitu ya Orebu ndi Zeebu kwa Gideoni tsidya lija la Yordani.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/7-17171600689ad907b37788d840bfdd1e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *