1 Ndipo amuna a Efuremu anati kwa iye, Ichi watichitira nchiyani, osatiitana popita iwe kulimbana ndi Amidiyani? Natsutsana naye kolimba.
2 Koma ananena nao, Ndachitanji tsopano monga inu? Kodi kukunkha mphesa kwa Efuremu sikuposa kutchera mphesa kwa Abiyezere?
3 Mulungu anapereka m’dzanja lanu akalonga a Midiyani, Orebu ndi Zeebu, ndipo ndinakhoza kuchitanji monga inu? Pamenepo mkwiyo wao unamlezera, atanena mau awa.
A ku Sukoti ndi a ku Penuwele anyoza Gideoni nalangidwa naye
4 Ndipo Gideoni anafika ku Yordani, naoloka, iye ndi amuna mazana atatu anali naye, ali otopa koma ali chilondolere.
5 Ndipo ananena kwa amuna a ku Sukoti, Mupatsetu anthu awa akunditsata mitanda yamkate; pakuti atopa, ndipo ndilikulondola Zeba ndi Zalimuna mafumu a Midiyani.
6 Koma akalonga a ku Sukoti anati, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna ali m’dzanja lako tsopano apa, kuti ife tiwaninkhe ankhondo ako mkate?
7 Ndipo Gideoni anati, Chifukwa chake, Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna m’dzanja langa, ndidzapuntha nyama yanu ndi minga ya m’chipululu ndi mitungwi.
8 Ndipo anachokapo kukwera ku Penuwele, nanena nao momwemo; ndipo amuna a ku Penuwele anamyankha monga adamyankha amuna a ku Sukoti.
9 Ndipo ananenanso kwa amuna a ku Penuwele ndi kuti, Ndikabwerera ndi mtendere ndidzagumula nsanja iyi.
10 Zeba ndi Zalimuna ndipo anali mu Karikori, ndi a m’misasa ao pamodzi nao, amuna monga zikwi khumi ndi zisanu; ndiwo otsala onse a khamu lonse la ana a kum’mawa; popeza atagwa amuna zikwi zana limodzi ndi makumi awiri akusolola lupanga.
11 Ndipo Gideoni anakwerera njira ya iwo okhala m’mahema kum’mawa kwa Noba, ndi Yogobeha, nakantha khamulo popeza khamulo linakhala lokhazikika mtima.
12 Ndipo Zeba ndi Zalimuna anathawa; koma anawatsata, nagwira mafumu awiri a Midiyani Zeba ndi Zalimuna, nanjenjemeretsa khamu lonse.
13 Pamenepo Gideoni mwana wa Yowasi anabwerera kunkhondo pokwerera pa Heresi.
14 Ndipo anagwira mnyamata wa anthu a ku Sukoti, nafunsira; ndipo anamsimbira akalonga a ku Sukoti, ndi akulu ake amuna makumi asanu ndi awiri kudza asanu ndi awiri.
15 Ndipo anafika kwa amuna a ku Sukoti, nati, Tapenyani Zeba ndi Zalimuna amene munanditonza nao ndi kuti, Kodi manja a Zeba ndi Zalimuna akhala m’dzanja lako, kuti tiwaninkhe mkate amuna ako akulema?
16 Ndipo anagwira akulu a m’mzinda ndi minga ya kuchipululu ndi mitungwi, nawalanga nazo amuna a ku Sukoti.
17 Ndipo anagamula nsanja ya Penuwele, napha amuna akumzinda.
18 Pamenepo anati kwa Zeba ndi Zalimuna, Amunawo munawapha ku Tabori anali otani? Iwo nayankha, Monga iwe momwemo iwowa; yense wakunga mwana wa mfumu.
19 Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.
20 Nati kwa Yetere mwana wake woyamba, Tauka, nuwaphe. Koma mnyamatayo sanasolole lupanga lake; pakuti anaopa, pokhala anali mnyamata.
21 Pamenepo Zeba ndi Zalimuna anati, Tauka iwe mwini nutigwere; pakuti monga munthu momwemo mphamvu yake. Ndipo Gideoni anauka nawapha Zeba ndi Zalimuna, nalanda mphande zinali kukhosi kwangamirazao.
Gideoni akana kulowa ufumu
22 Pamenepo anthu a Israele anati kwa Gideoni, Mutilamulire ndi inu, ndi mwana wanu, ndi mdzukulu wanu, pakuti mwatipulumutsa m’dzanja la Amidiyani.
23 Koma Gideoni ananena nao. Sindidzalamulira inu, ngakhale mwana wanga sadzalamulira inu; Yehova adzalamulira inu.
24 Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele.
25 Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo chovala, naponyamo yense maperere a mwa zofunkha zao.
26 Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao.
27 Ndipo Gideoni anawapanga fano, naliika m’mzinda mwake, ndiwo Ofura; ndi Israele yense analitsata kuligwadira pomwepo; ndipo linakhala kwa Gideoni ndi nyumba yake ngati msampha.
28 Motero anagonjetsa Amidiyani pamaso pa ana a Israele, osaweramutsanso mitu yao iwowa. Ndipo dziko lidapumula zaka makumi anai m’masiku a Gideoni.
29 Ndipo Yerubaala, mwana wa Yowasi anamuka, nakhala m’nyumba ya iye yekha.
30 Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.
31 Ndipo mkazi wake wamng’ono wokhala mu Sekemu, iyenso anambalira mwana wamwamuna; namutcha dzina lake Abimeleki.
32 Ndipo Gideoni mwana wa Yowasi anafa atakalamba bwino, naikidwa m’manda a Yowasi atate wake, mu Ofura wa Aabiyezere.
33 Ndipo kunali, atafa Gideoni, ana a Israele anabwereranso nagwadira Abaala, nayesa Baala-Beriti mulungu wao.
34 Ndi ana a Israele sanakumbukire Yehova Mulungu wao, amene anawapulumutsa m’dzanja la adani ao onse pozungulira ponse;
35 osachitira chifundo nyumba ya Yerubaala, ndiye Gideoni, monga mwa zokoma zonse iye anachitira Israele.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/8-a6be2e9727e28464d018e0d24de7334e.mp3?version_id=1068—