Mika ndi fano lake
1 Ndipo ku mapiri a Efuremu kunali munthu dzina lake ndiye Mika.
2 Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m’makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.
3 Nabwezera amake ndalama zija mazana khumi ndi limodzi; nati amai wake, Kupatula ndapatulira Yehova ndalamazo zichoke ku dzanja langa, zimuke kwa mwana wanga, kupanga nazo fano losema ndi fano loyenga; m’mwemo ndikubwezera izi.
4 Ndipo pamene anambwezera mai wake ndalamazo, mai wake anatapako ndalama mazana awiri, nazipereka kwa woyenga, ndiye anazipanga fano losema ndi fano loyenga; ndipo linakhala m’nyumba ya Mika.
5 Koma munthuyu Mika anali nayo nyumba ya milungu, napanga chovala cha wansembe, ndiaterafi, namninkha zansembe mwana wake wina wamwamuna, amene anakhala wansembe wake.
6 Masikuwa panalibe mfumu mu Israele, yense anachita chomuyenera m’maso mwake.
7 Ndipo panali mnyamata wa ku Betelehemu ku Yuda, wa banja la Yuda, ndiye Mlevi, nagonera iye komweko.
8 Adachokera munthuyo m’mudzi mu Betelehemu ku Yuda, kugonera paliponse akapeza pokhala; ndi pa ulendo wake anafika ku mapiri a Efuremu, kunyumba ya Mika.
9 Ndipo Mika ananena naye, Ufumira kuti? Nati kwa iye, Ndine Mlevi wa ku Betelehemu ku Yuda, ndilikumuka kugonera kumene ndikapeza pokhala.
10 Nanena naye Mika, Khalitsa nane, nukhale atate wanga, ndi wansembe wanga, ndipo ndidzakupatsa ndalama khumi pachaka, ndi chovala chofikira, ndi zakudya zako. Nalowa Mleviyo.
11 Ndi Mleviyo anavomera kukhalitsa ndi munthuyo; ndi mnyamatayo anamkhalira ngati mmodzi wa ana ake.
12 Ndipo Mika anamninkha zansembe Mleviyo, ndi mnyamatayo anakhala wansembe wake, nakhala m’nyumba ya Mika.
13 Nati Mika, Tsopano ndidziwa kuti Yehova adzandichitira chokoma, popeza ndili naye Mlevi akhale wansembe wanga.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JDG/17-59a84d5e6368e3c98c0f66ba33ef7c46.mp3?version_id=1068—