1 Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu chimwemwe changa ndi korona wanga, chilimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.
2 Ndidandaulira Yuwodiya, ndidandaulira Sintike, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.
3 Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m’goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m’buku la Moyo.
4 Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.
5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.
6 Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.
7 Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwaKhristuYesu.
8 Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
9 Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
Paulo ayamika Afilipi popeza adamtumiza zomthandizira
10 Koma ndinakondwera mwa Ambuye kwakukulu, kuti tsopano munatsitsimukanso kulingirira mtima za kwa ine, kumenekonso munalingirirako, koma munasowa pochitapo.
11 Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo.
12 Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m’zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.
13 Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.
14 Koma munachita bwino kuti munayanjana nane m’chisautso changa.
15 Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m’chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane naneMpingoumodzi wonse m’makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;
16 pakuti mu Tesalonikanso munanditumizira pa chosowa changa kamodzi kapena kawiri.
17 Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.
18 Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fungo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.
19 Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.
20 Ndipo kwa Mulungu ndi Atate wathu kukhale ulemerero kunthawi za nthawi,Amen.
21 Perekani moni kwa woyera mtima aliyense mwa Khristu Yesu. Abalewo akukhala ndi ine akupatsani moni.
22 Oyera mtima onse akupatsani inu moni, koma makamaka iwo a banja laKaisara.
23 Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PHP/4-407964e8d6b92417e3642b890fa40bbe.mp3?version_id=1068—