Angelo asanu ndi awiri ndi miliri isanu ndi iwiri
1 Ndipo ndinaona chizindikiro china m’mwamba, chachikulu ndi chozizwitsa,angeloasanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, ndiyo yotsiriza, kuti mwa iyo watsirizika mkwiyo wa Mulungu.
2 Ndipo ndinaona ngati nyanja yagalasi yosakaniza ndi moto; ndipo iwo amene anachigonjetsa chilombocho, ndi fano lake ndi chiwerengero cha dzina lake, anaimirira pa nyanja yagalasi, nakhala nao azeze a Mulungu.
3 Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo yaMwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.
4 Ndani adzakhala wosaopa ndi wosalemekeza dzina lanu Ambuye? Chifukwa Inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.
5 Ndipo zitatha izi ndinaona, ndipo panatseguka pa Kachisi wa chihema cha umboni mu Mwamba:
6 ndipo anatuluka mu Kachisi angelo asanu ndi awiri akukhala nayo miliri isanu ndi iwiri, atavala malaya woyera, ndi wonyezimira, namangira malamba agolide pachifuwa pao.
7 Ndipo chimodzi cha zamoyo zinai chinapatsa angelo asanu ndi awiri mbale zisanu ndi ziwiri zagolide zodzala ndi mkwiyo wa Mulungu wakukhala ndi moyo ku nthawi za nthawi.
8 Ndipo Kachisi anadzazidwa ndi utsi wochokera ku ulemerero wa Mulungu ndi ku mphamvu yake; ndipo palibe munthu anakhoza kulowa mu Kachisi kufikira ikatha miliri isanu ndi iwiri ya angelo asanu ndi awiri.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/REV/15-7a246e65a78609aef73c4c7b21eff11b.mp3?version_id=1068—