Categories
1 SAMUELE

1 SAMUELE 15

Saulo alamulidwa aononge Amaleke

1 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Yehova ananditumiza ine kukudzozani mukhale mfumu ya anthu ake Aisraele; chifukwa chake tsono mumvere kunena kwa mau a Yehova.

2 Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m’mene iye anakwera kutuluka mu Ejipito.

3 Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng’ombe ndi nkhosa,ngamirandi bulu.

4 Ndipo Saulo anamemeza anthu, nawawerenga ku Telaimu, akuyenda pansi zikwi mazana awiri, ndi a kwa Yuda anthu zikwi khumi.

5 Ndipo Saulo anafika kumzinda wa Amaleke, nalalira kuchigwa.

6 Ndipo Saulo anauza Akeni kuti, Mukani, chokani mutsike kutuluka pakati pa Aamaleke, kuti ndingakuonongeni pamodzi ndi iwo; pakuti inu munachitira ana a Israele onse zabwino, pakufuma iwo ku Ejipito. Chomwecho Akeni anachoka pakati pa Aamaleke.

7 Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.

8 Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.

9 Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng’ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafune kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse.

Samuele adzudzula Saulo pa kusamvera kwake

10 Pamenepo mau a Yehova anafika kwa Samuele, nati,

11 Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.

12 Ndipo Samuele analawirira m’mawa kuti akakomane ndi Saulo; ndipo munthu anamuuza Samuele kuti, Saulo anafika ku Karimele, ndipo taonani, anaimika chikumbutso chake, nazungulira, napitirira, natsikira ku Giligala.

13 Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova.

14 Ndipo Samuele anati, Koma tsono kulirako kwa nkhosa ndilikumva m’makutu anga, ndi kulirako kwa ng’ombe ndilikumva, nchiyani?

15 Ndipo Saulo anati, Anazitenga kwa Aamaleke; pakuti anthu anasunga nkhosa zokometsetsa ndi ng’ombe, kuzipereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu; koma zina tinaziononga konsekonse.

16 Pomwepo Samuele ananena ndi Saulo, Imani, ndidzakudziwitsani chimene Yehova wanena ndi ine usiku walero. Ndipo iyeyo anati kwa iye, Nenani.

17 Nati Samuele, M’mene munali wamng’ono m’maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.

18 Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konsekonse Aamaleke akuchita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.

19 Chifukwa ninji tsono simunamvere mau a Yehova, koma munathamangira zowawanya, ndi kuchita choipa pamaso pa Yehova?

20 Ndipo Saulo ananena ndi Samuele, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleke, ndi Aamaleke ndinawaononga konsekonse.

21 Koma anthuwo anatengako zowawanya, nkhosa ndi ng’ombe, zoposa za zija tidayenera kuziononga, kuziphera nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.

22 Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.

23 Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.

24 Ndipo Saulo anati kwa Samuele, Ndinachimwa; pakuti ndinalumpha lamulo la Yehova, ndi mau anu omwe; chifukwa ndinaopa anthuwo, ndi kumvera mau ao.

25 Chifukwa chake tsono, mukhululukire tchimo langa, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova.

26 Ndipo Samuele ananena ndi Saulo, Ine sindibwerera nanu; pakuti munakaniza mau a Yehova, ndipo Yehova anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu ya Israele.

27 Ndipo pakupotoloka Samuele kuti achoke, iye anagwira chilezi cha mwinjiro wake, ndipo chinang’ambika.

28 Ndipo Samuele ananena naye, Yehova anang’amba ufumu wa Israele lero kuuchotsa kwa inu, naupatsa kwa mnansi wanu wina wabwino woposa inu.

29 Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.

30 Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.

31 Chomwecho Samuele anabwerera natsata Saulo; ndi Saulo analambira Yehova.

32 Ndipo Samuele anati, Bwerani naye kwa ine kuno Agagi mfumu ya Aamaleke. Ndipo Agagi anabwera kwa iye mokondwera. Nati Agagi, Zoonadi kuwawa kwa imfa kunapitirira.

33 Ndipo Samuele anati, Monga lupanga lako linachititsa akazi ufedwa, momwemo mai wako adzakhala mfedwa mwa akazi. Ndipo Samuele anamdula Agagi nthulinthuli pamaso pa Yehova ku Giligala.

34 Pamenepo Samuele ananka ku Rama; ndi Saulo anakwera kunka kunyumba yake ku Gibea wa Saulo.

35 Ndipo Samuele sanadzenso kudzaona Saulo kufikira tsiku la imfa yake; koma Samuele analira chifukwa cha Saulo; ndipo Yehova anali ndi chisoni kuti anamlonga Saulo mfumu ya Israele.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/15-11f48f1ca6cd8d83a51e6798fd489228.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *