1 Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m’malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m’dzanja lake.
2 Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.
3 Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala.
4 Ndipo anauza Saulo kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunenso.
5 Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kuminda, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji mu mzinda wachifumu pamodzi ndi inu?
6 Ndipo Akisi anampatsa Zikilagi tsiku lomweli; chifukwa chake Zikilagi ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.
7 Ndipo kuwerenga kwake kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko chaka chimodzi ndi miyezi inai.
8 Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m’dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.
9 Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunge ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng’ombe, ndi abulu, ndingamira, ndi zovala; nabwera nafika kwa Akisi.
10 Ndipo Akisi anati, Waponyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameele, ndi a kumwera kwa Akeni.
11 Ndipo Davide sadasunge wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.
12 Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati, Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israele, chifukwa chake iye adzakhala mnyamata wanga chikhalire.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1SA/27-af70c510ae202128647983831e70ed96.mp3?version_id=1068—