Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 11

Tchimo loopsa la Davide

1 Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira kuYerusalemu.

2 Ndipo kunali pa madzulo Davide anauka pa kama wake nayenda pa tsindwi la nyumba ya mfumu. Ndipo iye ali patsindwipo anaona mkazi alinkusamba; ndi mkaziyo anali wochititsa kaso pomuyang’ana.

3 Ndipo Davide anatumiza munthu nafunsa za mkaziyo. Ndipo wina anati, Sindiye Bateseba, mwana wamkazi wa Eliyamu, mkazi wa Uriya Muhiti?

4 Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake.

5 Ndipo mkaziyo anaima, natumiza munthu nauza Davide, kuti Ndili ndi pakati.

6 Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide.

7 Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji?

8 Ndipo Davide anauza Uriya, Utsikire kunyumba yako, nutsuke mapazi ako. Ndipo Uriya anachoka kunyumba ya mfumu, ndipo anamtsata munthu ndi mphatso ya mfumu.

9 Koma Uriya anagona pa khomo la nyumba ya mfumu pamodzi ndi anyamata onse a mbuye wake, osatsikira kunyumba yake.

10 Ndipo pamene anauza Davide kuti, Uriya sanatsikire kunyumba yake, Davide ananena ndi Uriya, Kodi sunabwere kuulendo? Chifukwa ninji sunatsikire kunyumba yako?

11 Uriya nanena ndi Davide, Likasalo, ndi Israele, ndi Yuda, alikukhala m’misasa, ndi mbuye wanga Yowabu, ndi anyamata a mbuye wanga alikugona kuthengo, potero ndikapita ine kodi kunyumba yanga kuti ndidye, ndimwe, ndigone ndi mkazi wanga? Pali inu, pali moyo wanu, sindidzachita chinthuchi.

12 Ndipo Davide anati kwa Uriya, Utsotse pano leronso, ndipo mawa ndidzakulola umuke. Chomwecho Uriya anakhala ku Yerusalemu tsiku lomwelo ndi m’mawa mwake.

13 Ndipo pakumuitana Davide, iyeyo anadya namwa pamaso pake; Davide namledzeretsa; ndipo usiku anatuluka kukagona pa kama wake pamodzi ndi anyamata a mbuye wake; koma sanatsikire kunyumba yake.

14 Ndipo m’mawa Davide analembera Yowabu kalata, wopita naye Uriya.

15 Ndi m’kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe.

16 Ndipo Yowabu atayang’anira mzindawo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi.

17 Ndipo akumzindawo anatuluka, namenyana ndi Yowabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Muhiti anafanso.

18 Pamenepo Yowabu anatumiza munthu nauza Davide zonse za nkhondoyi;

19 nauza mthengawo kuti, Utatsiriza kuuza mfumu zonse za nkhondozo;

20 kudzali kuti ukapsa mtima wa mfumu nikati kwa iwe, Chifukwa ninji munayandikira pafupi potere pamzinda kukamenyana nao? Simunadziwe kodi kuti apalingawo adzaponya?

21 Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa.

22 Chomwecho mthengawo unamuka, nufika, nudziwitsa Davide zonse Yowabu anamtumiza.

23 Ndipo mthengawo unati kwa Davide, Anthuwo anatipambana natulukira kwa ife kumundako, koma tinawagwera kufikira polowera kuchipata.

24 Ndipo akuponyawo amene anali palinga anaponya anyamata anu; ndipo anyamata ena a mfumu anafa, ndi mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso anafa.

25 Pomwepo Davide ananena ndi mthengawo, Udzatero kwa Yowabu, Chisakuipire ichi, lupanga limaononga wina ndi mnzake. Onjeza kulimbitsa nkhondo yako pamzindapo, nuupasule; numlimbikitse motere.

26 Ndipo pamene mkazi wa Uriya anamva kuti Uriya mwamuna wake adamwalira, iye analira maliro a mwamuna wake.

27 Ndipo pakutuluka malirowo, Davide anatumiza munthu namtenga afike kwao kunyumba yake; ndipo iyeyo anakhala mkazi wake nambalira mwana wamwamuna. Koma Yehova anaipidwa ndi chinthu chimene Davide adachita.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/11-6a0d04077c2178b20367a98d71b1071c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *