Categories
2 SAMUELE

2 SAMUELE 23

Nyimbo yotsiriza ya Davide

1 Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:

Atero Davide mwana wa Yese,

atero munthu wokwezedwa,

ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,

ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.

2 Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,

ndi mau ake anali pa lilime langa.

3 Mulungu wa Israele anati,

Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine;

kudzakhala woweruza anthu molungama;

woweruza m’kuopa Mulungu.

4 Iye adzakhala ngati kuunika kwa m’mawa,

potuluka dzuwa, M’mawa mopanda mitambo;

pamene msipu uphuka kutuluka pansi,

chifukwa cha kuwala koyera, italeka mvula.

5 Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu;

koma Iye anapangana ndi ine pangano losatha,

lolongosoka mwa zonse ndi losungika;

pakuti ichi ndi chipulumutso changa chonse,

ndi kufuma kwanga konse,

kodi sadzachimeretsa?

6 Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,

pakuti siigwiridwa ndi dzanja;

7 koma wakukhudza iyo adzikonzeratu chitsulo ndi luti la mkondo;

ndipo idzatenthedwa konse ndi moto m’malo mwao.

Angwazi a Davide

8 Maina a ngwazi Davide anali nazo ndiwo: Yosebu-Basebeti Mtakemoni, mkulu wa akazembe; ameneyu ndiye Adino Mwezni wolimbana ndi mazana atatu ophedwa nthawi imodzi.

9 Ndipo wotsatana naye Eleazara mwana wa Dodo mwana wa Mwahohi, mmodzi wa ngwazi zitatu zokhala ndi Davide pamene iwo anatonza Afilisti osonkhanidwa kunkhondo kumeneko, atachoka Aisraele;

10 iye ananyamuka, nakantha Afilisti kufikira dzanja lake linalema, ndi dzanja lake lomamatika kulupanga; ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu tsiku lija, ndipo anthu anabwera m’mbuyo mwake kukafunkha kokha.

11 Ndipo wotsatana naye ndiye Sama mwana wa Age Muharari. Ndipo Afilisti anasonkhana ali gulu pa Lehi pamene panali munda wamphodza; anthu nathawa Afilistiwo.

12 Koma iyeyo anaima pakati pamundawo, nautchinjiriza, napha Afilistiwo. Ndipo Yehova anachititsa chipulumutso chachikulu.

13 Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m’phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m’chigwa cha Refaimu.

14 Pamenepo Davide anali m’linga, ndi boma la Afilisti linali mu Betelehemu.

15 Ndipo Davide analakalaka nati, Ha! Wina akadandipatsa madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu chili pachipatapo!

16 Ndipo ngwazi zitatuzo zinapyola khamu la Afilisti, ndipo zinatunga madzi m’chitsime cha ku Betelehemu, cha pa chipatacho, nawatenga, nafika nao kwa Davide; koma iye sanafune kumwako, koma anawathira pansi kwa Yehova.

17 Nati, Ndisachite ichi ndi pang’ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi.

18 Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

19 Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikane ndi atatu oyamba.

20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m’mbuna nyengo ya chipale chofewa;

21 ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m’dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m’dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

22 Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.

23 Iye ndiye waulemu koposa makumi atatuwo, koma sadafikane ndi atatu oyamba. Ndipo Davide anamuika kuyang’anira olindirira ake.

24 Asahele mbale wa Yowabu anali wa makumi atatuwo; Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu;

25 Sama Mharodi, Elika Mharodi;

26 Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi Mtekowa.

27 Abiyezere Mwanatoti, Mebunai Muhusa;

28 Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa;

29 Helebi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibea wa ana a Benjamini;

30 Benaya Mpiratoni, Hidai wa ku timitsinje ta Gaasi;

31 Abiyaliboni Mwarabati, Azimaveti Mbahurimi;

32 Eliyaba Msaaliboni wa ana a Yaseni, Yonatani;

33 Sama Muharari, Ahiyamu mwana wa Sarara Muharari;

34 Elifeleti mwana wa Ahasibai, mwana wa Mmaaka, Eliyamu mwana wa Ahitofele Mgiloni;

35 Heziro wa ku Karimele, Paarai Mwaraba;

36 Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, Bani Mgadi;

37 Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti, onyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya;

38 Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri;

39 Uriya Muhiti; onse pamodzi anali makumi atatu mphambu asanu ndi awiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2SA/23-8ccdfe58f58a58338ec50c7f9a340fd8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *