Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 1

Ukalamba wa Davide, atchula Solomoni wodzalowa m’malo mwake

1 Ndipo mfumu Davide anakalamba nachuluka masiku ake; ndipo iwo anamfunda ndi zofunda, koma iye sanafundidwe.

2 Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m’mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

3 Tsono anafunafuna m’malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.

4 Ndipo namwaliyo anali wokongola ndithu, namasunga mfumu namtumikira; koma mfumu sinamdziwe.

5 Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.

6 Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.

7 Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.

8 Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natanimneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.

9 Ndipo Adoniya anapha nkhosa ndi ng’ombe ndi nyama zonona pamwala pa Zoheleti, uli pafupi ndi chitsime cha Rogele, naitana abale ake onse ana a mfumu, ndi anthu onse a Yuda anyamata a mfumu;

10 koma Natani mneneriyo, ndi Benaya, ndi anthu amphamvu aja, ndi Solomoni mbale wake, sanawaitane.

11 Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?

12 Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni.

13 Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirire mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?

14 Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.

15 Pamenepo Bateseba analowa kwa mfumu kuchipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.

16 Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?

17 Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.

18 Ndipo tsopano taonani, Adoniya walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.

19 Ndipo iye anapha ng’ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi Abiyatara wansembe, ndi Yowabu kazembe wa nkhondo; koma Solomoni mnyamata wanu sanamuitane.

20 Ndipo tsopano, mbuye wanga mfumu, maso a Aisraele onse ali pa inu, kuti muwauze amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye.

21 Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa.

22 Ndipo taona, iye ali chilankhulire ndi mfumu, Natani mneneriyo analowamo.

23 Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.

24 Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu?

25 Popeza iye watsika lero, nakapha ng’ombe ndi nyama zonona ndi nkhosa zaunyinji, naitana ana aamuna onse a mfumu, ndi akazembe a nkhondo, ndi Abiyatara wansembe; ndipo taonani, iwowo akudya ndi kumwa pamaso pake, nati, Akhale ndi moyo mfumu Adoniya.

26 Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane.

27 Chinthu ichi chachitika ndi mbuye wanga mfumu kodi, ndipo simunadziwitse mnyamata wanu amene adzakhala pa mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu atamuka iye?

28 Tsono mfumu Davide anayankha, nati, Ndiitanireni Bateseba. Ndipo iye analowa pamaso pa mfumu, naima pamaso pa mfumu.

29 Ndipo mfumu inalumbira, niti, Pali Yehova amene anapulumutsa moyo wanga m’nsautso monse,

30 zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m’malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.

31 Pamenepo Bateseba anaweramitsa pansi nkhope yake, nalambira mfumu, nati, Mbuye wanga mfumu Davide akhale ndi moyo nthawi zamuyaya.

32 Ndipo mfumu Davide anati, Kandiitanireni Zadoki wansembeyo, ndi Natani mneneriyo, ndi Benaya mwana wa Yehoyada. Iwo nalowa pamaso pa mfumu.

33 Ndipo mfumu inati kwa iwo, Tengani akapolo a mfumu yanu, nimukweze Solomoni mwana wanga pa nyuru yangayanga, nimutsikire naye ku Gihoni.

34 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri akamdzoze kumeneko akhale mfumu ya Israele; ndipo muombe lipenga, ndi kuti, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.

35 Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m’malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda.

36 Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu, nati, Amen, ateronso Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu.

37 Monga umo Yehova anakhalira ndi mbuye wanga mfumu momwemo akhalenso ndi Solomoni, nakuze mpando wake wachifumu upose mpando wachifumu wa mbuye wanga mfumu Davide.

38 Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.

39 Ndipo Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta inali mu Chihema, namdzoza Solomoni. Ndipo iwo anaomba lipenga, ndi anthu onse anati, Mfumu Solomoni akhale ndi moyo.

40 Ndipo anthu onse anakwera namtsata, naliza zitoliro, nakondwera ndi kukondwera kwakukulu, kotero kuti pansi panang’ambika ndi phokoso lao.

41 Ndipo Adoniya ndi oitanidwa onse anali ndi iye analimva atatha kudya. Ndipo Yowabu, pakumva kuomba kwa lipengalo, anati, Phokosolo ndi chiyani kuti m’mzinda muli chibumo?

42 Iye akali chilankhulire, taona, walowa Yonatani mwana wa Abiyatara wansembe, ndipo Adoniya anati, Lowa, popeza ndiwe munthu wamphamvu, nubwera nao uthenga wabwino.

43 Ndipo Yonatani anayankha, nati kwa Adoniya, Zedi Davide mbuye wathu mfumu walonga Solomoni ufumu:

44 ndipo mfumu yatumanso Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja, namkweza iye pa nyuru ya mfumu.

45 Ndipo Zadoki wansembe ndi Natani mneneri anamdzoza mfumu ku Gihoni, ndipo achokera kumeneko chikondwerere, ndi m’mzindamo muli phokoso. Ndilo phokoso limene mwamvali.

46 Ndiponso Solomoni wakhala pa chimpando cha ufumu.

47 Ndiponso akapolo a mfumu anadzadalitsa Davide mbuye wathu mfumu, nati, Mulungu wanu aposetse dzina la Solomoni lipunde dzina lanu, nakulitse mpando wake wachifumu upose mpando wanu wachifumu; ndipo mfumu anawerama pakamapo.

48 Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israele, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wachifumu, maso anga ali chipenyere.

49 Pamenepo oitanidwa onse a Adoniya anachita mantha, nanyamuka, napita yense njira yake.

50 Ndipo Adoniya anaopa chifukwa cha Solomoni, nanyamuka, nakagwira nyanga za guwa la nsembe.

51 Ndipo anthu anakauza Solomoni, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomoni, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomoni alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wake ndi lupanga.

52 Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.

53 Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/1-7c2571e08ed067f26ea7991072da72b6.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *