Categories
1 MAFUMU

1 MAFUMU 6

Za mamangidwe a Kachisi

1 Ndipo kunachitika zitapita zaka mazana anai mphambu makumi asanu ndi atatu atatuluka ana a Israele m’dziko la Ejipito, chaka chachinai chakukhala Solomoni mfumu ya Israele, m’mwezi wa Zivi, ndiwo mwezi wachiwiri, iye anayamba kumanga nyumba ya Yehova.

2 Ndipo nyumbayo mfumu Solomoni anaimangira Yehova, m’litali mwake munali mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi m’mimba mwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu.

3 Ndipo anamanga chipinda cholowera pakhomo pa nyumba ya Kachisiyo, m’litali mwake munali mikono makumi awiri monga m’mimba mwake mwa nyumbayo, kupingasa kwake kunali mikono khumi ku khomo la nyumba.

4 Ndipo m’nyumbamo anamanga mazenera a sefa wokhazikika.

5 Ndipo anamanga zipinda zosanjikizana zogundana ndi khoma, kuzungulira makoma a nyumba ya Kachisi, ndi chipinda chamkati; namanga zipinda zozinga.

6 Chipinda chapansicho kupingasa kwake kunali mikono isanu, chapakaticho kupingasa kwake mikono isanu ndi umodzi, chachitatucho kupingasa kwake mikono isanu ndi iwiri; pakuti kubwalo anachepsa khoma pozungulirapo, mitanda isalongedwe m’makoma a nyumba.

7 Ndipo nyumbayo pomangidwa inamangidwa ndi miyala yokonzeratu asanaitute; ndipo m’nyumbamo simunamveke kulira nyundo, kapena nkhwangwa, kapena chipangizo chachitsulo, pomangidwa iyo.

8 Khomo lolowera m’zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kufikira ku zipinda za pakati, ndi kutuluka m’zapakatizo kulowa m’zachitatuzo.

9 Momwemo anamanga nyumbayo naitsiriza, naika mitanda, naifolera ndi matabwa amikungudza.

10 Ndipo anamanga zipindazo zogundana ndi nyumba yonseyo, chipinda chilichonse msinkhu wake mikono isanu; ndipo anazilumikizitsa kunyumba ndi mitengo yamkungudza.

11 Ndipo mau a Yehova anafika kwa Solomoni, nati,

12 Kunena za nyumba ino ulikuimanga, ukamayenda iwe m’malemba anga, ndi kumachita maweruzo anga, ndi kumasunga malamulo anga onse kuyendamo, pamenepo Ine ndidzakhazikitsira iwe mau anga amene ndinauza Davide atate wako.

13 Ndipo ndidzakhala pakati pa ana a Israele osawasiya anthu anga a Israele.

14 Tsono Solomoni anamanga nyumbayo naitsiriza.

15 Ndipo anatchinga makoma a nyumba m’katimo ndi matabwa amkungudza, kuyambira pansi kufikira posanja, natchinga m’katimo ndi matabwa, nayala pansi m’nyumbamo matabwa amlombwa.

16 Ndipo anadulitsa ndi matabwa amkungudza mikono makumi awiri m’kati mwa nyumba m’tsogolo mwake, kuyambira pansi kulekeza kumitanda; ichi anamanga kukhala chipinda chamkati, malo opatulika kwambiri.

17 Ndipo nyumbayo, ndiyo Kachisi wa kutsogolo kwa chipindacho, inali ya mikono makumi anai.

18 Ndipo m’kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gadaa; munali mikungudza yokhayokha simunaoneke mwala ai.

19 Ndipo anakonza m’kati mwa nyumba m’tsogolo mwake, kuikamolikasa la chipanganola Yehova.

20 Ndipo m’kati mwa chipindacho, m’litali mwake munali mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golide wayengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza.

21 Momwemo Solomoni anakuta m’kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide.

22 Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golide mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali chakuno cha chipinda chamkati analikuta ndi golide.

23 Ndipo m’chipinda chamkatimo anasema mitengo yaazitonaakerubiawiri, yense wa msinkhu wake mikono khumi.

24 Ndipo phiko limodzi la kerubi linali la mikono isanu, ndi phiko lina la kerubi linalinso la mikono isanu; kuyambira ku nsonga ya phiko limodzi kufikira ku nsonga ya phiko lina inali mikono khumi.

25 Ndi kerubi winayo msinkhu wake unali mikono khumi; akerubi onse awiri anafanana muyeso wao ndi msinkhu wao.

26 Msinkhu wa kerubi mmodzi unali mikono khumi, ndi wa kerubi wina momwemo.

27 Ndipo anaika akerubiwo m’chipinda cha m’katimo, ndi mapiko a akerubiwo anatambasuka kotero kuti phiko lake la kerubi mmodzi linajima ku khoma limodzi, ndipo phiko la kerubi wina linajima khoma lina, ndi mapiko ao anagundana pakati pa nyumba.

28 Ndipo anawakuta akerubi ndi golide.

29 Nalemba m’makoma onse akuzinga chipinda mafano olemba ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, m’katimo ndi kumbuyo kwake.

30 Ndipo anakuta ndi golide pansi pake pa nyumba m’katimo ndi kunja.

31 Ndipo pa khomo la chipinda chamkati anapanga zitseko za mtengo wa azitona, chitando cha khomolo chinali limodzi la magawo asanu a khoma lake.

32 Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo wa azitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nawakuta ndi golide; inde anakutanso ndi golide akerubi ndi migwalangwayo.

33 Momwemo anapanganso mphuthu za azitona za pa khomo la Kachisi, chitando chake chinali limodzi la magawo anai a khoma;

34 ndi zitseko ziwiri za mitengo yamlombwa pa khomo lina; panali chitseko chopatukana, ndi pa linzake panali chitseko chopatukana.

35 Ndipo analembapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gadaa, nakuta zolembazo ndi golide wopsapsala.

36 Ndipo bwalo la m’kati analimanga mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza.

37 Maziko ake a nyumba ya Yehova anaikidwa m’chaka chachinai m’mwezi wa Zivi.

38 Ndipo m’chaka chakhumi ndi chimodzi m’mwezi wa Buli ndiwo mwezi wachisanu ndi chitatu anatsiriza nyumba konsekonse monga mwa mamangidwe ake onse. Momwemo anaimanga zaka zisanu ndi ziwiri.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1KI/6-e86176dddbb0248d3de17d427c6ab100.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *