Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 1

Eliya ndi nthenda ya Ahaziya

1 Ndipo atamwalira Ahabu, Mowabu anapandukana ndi Israele.

2 Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pamwamba pa chipinda chake chosanja chinali ku Samariya, nadwala, natuma mithenga, nanena nayo, Mufunsire kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni ngati ndidzachira nthenda iyi.

3 Koma mthenga wa Yehova anati kwa Eliya wa ku Tisibe, Nyamuka, kwera kukomana ndi mithenga ya mfumu ya Samariya, nunene nayo, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti mukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni?

4 Chifukwa chake atero Yehova, Sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu. Nachoka Eliya.

5 Ndipo mithenga inabwerera kwa iye, nanena nayo, Mwabwerera chifukwa ninji?

6 Ndipo inanena naye, Munthu anakwera kukomana nafe, nati kwa ife, Kabwerereni kwa mfumu imene inakutumani inu, nimunene nayo, Atero Yehova, Kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele, kuti ulikutuma kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

7 Ndipo iye ananena nayo, Nanga maonekedwe ake a munthu anakwerayo kukomana nanu, nanena nanu mau awa, ndi otani?

8 Ninena naye, Ndiye munthu wovala zaubweya, namangira m’chuuno mwake ndi lamba lachikopa. Nati iye, Ndiye Eliya wa ku Tisibe.

9 Pamenepo mfumu inatuma kwa iye asilikali makumi asanu ndi mtsogoleri wao. Iye nakwera kunka kwa Eliya; ndipo taonani, analikukhala pamwamba paphiri. Ndipo analankhula naye, Munthu wa Mulungu iwe, mfumu ikuti, Tsika.

10 Nayankha Eliya, nanena ndi mtsogoleriyo, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo unatsika moto kumwamba, nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake.

11 Ndipo anabwereza kutuma kwa iye mtsogoleri wina ndi makumi asanu ake. Ndipo iye anayankha nanena naye, Munthu wa Mulungu iwe, itero mfumu, Tsika msanga.

12 Nayankha Eliya, nanena nao, Ndikakhala ine munthu wa Mulungu, utsike moto wakumwamba, nunyeketse iwe ndi makumi asanu ako. Pamenepo moto wa Mulungu unatsika kumwamba nunyeketsa iye ndi makumi asanu ake.

13 Ndipo anabwerezanso kutuma mtsogoleri wachitatu ndi makumi asanu ake. Nakwera mtsogoleri wachitatuyo, nadzagwada ndi maondo ake pamaso pa Eliya, nampembedza, nanena naye, Munthu wa Mulungu inu, ndikupemphani, moyo wanga ndi moyo wa anyamata anu makumi asanu awa akhale a mtengo wake pamaso panu.

14 Taonani, watsika moto wakumwamba, nunyeketsa atsogoleri awiri oyamba aja pamodzi ndi makumi asanu ao; koma tsopano moyo wanga ukhale wa mtengo wake pamaso panu.

15 Pamenepo mthenga wa Yehova anati kwa Eliya, Tsika naye, usamuopa. Nanyamuka iye, natsikira naye kwa mfumu.

16 Ndipo ananena nayo, Atero Yehova, Popeza watuma mithenga kukafunsira kwa Baala-Zebubi mulungu wa ku Ekeroni, kodi ndi popeza palibe Mulungu mwa Israele kufunsira mau ake? Chifukwa chake sudzatsika pakama pamene wakwerapo, koma udzafa ndithu.

17 Motero anafa monga mwa mau a Yehova adanena Eliyawo. Ndipo Yehoramu analowa ufumu m’malo mwake chaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya Yuda, pakuti analibe mwana wamwamuna.

18 Machitidwe ake ena tsono adawachita Ahaziya, sanalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Israele?

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/1-5866a6817fc93d2a14a902eeedc21d07.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *