Categories
2 MAFUMU

2 MAFUMU 4

Elisa achulukitsa mafuta a mkazi wamasiye

1 Ndipo wina wa akazi a ana a aneneri anafuula kwa Elisa, ndi kuti, Mnyamata wanu, mwamuna wanga wafa; mudziwa kuti mnyamata wanu anaopa Yehova; ndipo wafika wamangawa kunditengera ana anga awiri akhale akapolo ake.

2 Ndipo Elisa anati kwa iye, Ndikuchitire chiyani? Undiuze m’nyumba mwako muli chiyani? Nati, Mdzakazi wanu alibe kanthu m’nyumba, koma mtsuko wa mafuta.

3 Pamenepo anati, Kabwereke zotengera kwina kwa anansi ako onse, zotengera zopanda kanthu, zisakhale pang’ono.

4 Nulowe, nudzitsekere wekha ndi ana ako aamuna ndi kutsanulira m’zotengera zonsezi, nuike padera zodzalazo.

5 Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake aamuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.

6 Ndipo kunali, zitadzala zotengera, anati kwa mwana wake, Nditengere chotengera china. Nanena naye, Palibe chotengera china. Ndipo mafuta analeka.

7 Pamenepo anadza, namfotokozera munthu wa Mulungu. Nati iye, Kagulitse mafuta, ukabwezere mangawa ako, ndi zotsalapo zikusunge iwe ndi ana ako.

Mkazi wa ku Sunemu ndi mwana wake

8 Ndipo linafika tsiku lakuti Elisa anapitirira kunka ku Sunemu, kumeneko kunali mkazi womveka; ameneyo anamuumiriza adye mkate. Potero pomapitirako iyeyo, ankawapatukirako kukadya mkate.

9 Ndipo mkaziyo anati kwa mwamuna wake, Taona, tsopano ndidziwa kuti munthu uyu wakupitira pathu pano chipitire ndiye munthu woyera wa Mulungu.

10 Timmangire kachipinda kosanja, timuikirenso komweko kama, ndi gome, ndi mpando, ndi choikaponyali; ndipo kudzatero kuti akatidzera alowe m’mwemo.

11 Ndipo linadza tsiku lakuti anafikako, nalowa m’chipinda chosanja, nagona komweko.

12 Nati kwa Gehazi mnyamata wake, Itana Msunamu uja. Namuitana, naima mkaziyo pamaso pake.

13 Ndipo anati kwa iye, Ufunse mkaziyu tsopano, kuti, Taona watisungira ndi kusamalira uku konse; nanga tikuchitire iwe chiyani? Kodi tikunenere kwa mfumu, kapena kwa kazembe wa nkhondo? Koma anati, Ndikhala ine pakati pa anthu a mtundu wanga.

14 Pamenepo anati, Nanga timchitire iye chiyani? Nati Gehazi, Zedi alibe mwana, ndi mwamuna wake wakalamba.

15 Nati, Kamuitane. Namuitana, naima pakhomo mkaziyo.

16 Ndipo anati, Nyengo ino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.

17 Ndipo mkaziyo anaima, naona mwana wamwamuna nyengo yomweyo chaka chimene chija Elisa adanena naye.

18 Ndipo atakula mwanayo, linadza tsiku lakuti anatuluka kunka kwa atate wake, ali kwa omweta tirigu.

19 Nati kwa atate wake, Mutu wanga, mutu wanga! Pamenepo anati kwa mnyamata, Umnyamule umuke naye kwa amake.

20 Namnyamula, napita naye kwa amake. Ndipo anakhala pa maondo ake kufikira usana, namwalira.

21 Ndipo anakwera, namgoneka pa kama wa munthu wa Mulungu, natuluka, namtsekera.

22 Naitana mwamuna wake, nati, Nditumizire mmodzi wa anyamata ndi bulu mmodzi, kuti ndithamangire kwa munthu uja wa Mulungu, ndi kubweranso.

23 Ndipo anati, Ulikumuka kwa iye lero chifukwa ninji? Ngati mwezi wakhala, kapena mpaSabata? Koma anati, Kuli bwino.

24 Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.

25 Potero anamuka, nafika kwa munthu wa Mulungu kuphiri la Karimele. Ndipo kunali, pakumuona munthu wa Mulungu alinkudza kutali, anati kwa Gehazi mnyamata wake, Tapenya, suyo Msunamu uja;

26 uthamange tsopano kukomana naye, nunene naye, Muli bwino kodi? Mwamuna wanu ali bwino? Mwanayo ali bwino? Ndipo anati, Ali bwino.

27 Ndipo pofika kwa munthu wa Mulungu kuphiri anamgwira mapazi. Ndipo Gehazi anayandikira kuti amkankhe; koma munthu wa Mulungu anati, Umleke, pakuti mtima wake ulikumuwawa; ndipo Yehova wandibisira osandiuza ichi.

28 Ndipo mkaziyo anati, Ngati ndinapempha mwana kwa mbuyanga? Kodi sindinati, Musandinyenga?

29 Pamenepo anati kwa Gehazi, Udzimangire m’chuuno, nutenge ndodo yanga m’dzanja lako, numuke; ukakomana ndi munthu usampatse moni; wina akakupatsa moni usamyankhe; ukaike ndodo yanga pankhope pa mwanayo.

30 Koma make wa mwana anati, Pali Yehova, pali inunso, ngati nkukusiyani. Ndipo ananyamuka, namtsata.

31 Nawatsogolera Gehazi, naika ndodo pankhope pa mwanayo; koma mwanayo analibe mau, kapena kusamalira. Motero anabwerera kukomana naye, namuuza kuti, Sanauke mwanayo.

32 Ndipo pamene Elisa analowa m’nyumba, taonani, mwanayo ngwakufa, adamgoneka pakama pake.

33 Nalowa Elisa, nadzitsekera awiriwa, napemphera kwa Yehova.

34 Nakwera, nagona pa mwanayo ndi kulinganiza pakamwa pake ndi pakamwa pake, maso ake ndi maso ake, zikhato zake ndi zikhato zake, nadzitambasula pa iye, ndi mnofu wa mwana unafunda.

35 Pamenepo anabwera nayenda m’nyumba, chakuno kamodzi, chauko kamodzi; nakwera, nadzitambasuliranso pa iye; ndi mwana anayetsemula kasanu ndi kawiri, natsegula mwanayo maso ake.

36 Pamenepo anaitana Gehazi, nati, Kaitane Msunamu uja. Namuitana. Ndipo atalowa kuli iye, anati, Nyamula mwana wako.

37 Iye nalowa, nagwa pa mapazi ake, nadziweramitsa pansi; nanyamula mwana wake, natuluka.

Muli imfa m’nkhalimo

38 Ndipo Elisa anabwera ku Giligala, koma m’dzikomo munali njala; ndi ana a aneneri anali kukhala pansi pamaso pake; ndipo anati kwa mnyamata wake, Ika nkhali yaikuluyo, uphikire ana a aneneri.

39 Natuluka wina kukatchera ndiwo kuthengo, napeza chonga ngati mpesa, natcherapo zipuzi kudzaza m’funga mwake, nadza, nazichekerachekera m’nkhali ya chakudya, popeza sanazidziwe.

40 Pamenepo anagawira anthu kuti adye. Koma kunali, pakudya chakudyacho, anafuula nati, Munthu wa Mulungu, muli imfa m’nkhalimo. Ndipo sanathe kudyako.

41 Pamenepo anati, Bwera naoni ufa. Nathira m’nkhalimo; nati, Gawirani anthu kuti adye. Ndipo m’nkhalimo munalibe chowawa.

Mikate makumi awiri ikwanira anthu ambiri

42 Ndipo anadza munthu kuchokera ku Baala-Salisa, nabwera nayo m’thumba mikate ya zipatso zoyamba kwa munthu wa Mulungu, mikate ya barele makumi awiri, ndi ngala zaziwisi za tirigu zosaomba. Ndipo anati, Uwapatse anthu kuti adye.

43 Koma mnyamata wake anati, Chiyani? Ndigawire amuna zana ichi kodi? Koma anati, Uwapatse anthu kuti adye; pakuti atero Yehova, Adzadya nadzasiyako.

44 Potero anawagawira, nadya, nasiyapo, monga mwa mau a Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/4-95c655919329f382124d2077541740fb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *