Yowasi akonza Kachisi
1 Chaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi analowa ufumu wake; nakhala mfumu muYerusalemuzaka makumi anai; ndi dzina la mai wake ndiye Zibiya wa ku Beereseba.
2 Ndipo Yowasi anachita zoongoka pamaso pa Yehova masiku ake onse, m’mene anamlangizira wansembe Yehoyada.
3 Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza kumisanje.
4 Ndipo Yowasi anati kwa ansembe, Landirani ndalama zonse za zinthu zopatulika azibwera nazo kunyumba ya Yehova, ndizo ndalama za otha msinkhu, ndalama za munthu aliyense monga adamuyesa, ndi ndalama zimene yense azikumbuka m’mtima mwake kuti abwere nazo kunyumba ya Yehova.
5 Ansembe azilandire yense kwa iye amene adziwana naye, akonze nazo mogamuka nyumba, paliponse akapeza pogamuka.
6 Koma kunali, chaka cha makumi awiri mphambu zitatu cha mfumu Yowasi, ansembe sanathe kukonza mogamuka nyumba.
7 Pamenepo mfumu Yowasi anaitana Yehoyada wansembe, ndi ansembe ena, nanena nao, Mulekeranji kukonza mogamuka nyumba? Tsono musalandiranso ndalama kwa anzanu odziwana nao, kuziperekera mogamuka nyumba.
8 Navomera ansembe kusalandiranso ndalama za anthu, kapena kukonza mogamuka nyumba.
9 Ndipo Yehoyada wansembe anatenga bokosi, naboola chiboo pa chivundikiro chake, naliika pafupi paguwa la nsembe, ku dzanja lamanja polowera nyumba ya Yehova; ndipo ansembe akusunga pakhomo anaikamo ndalama zonse anabwera nazo anthu kunyumba ya Yehova.
10 Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m’bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m’matumba, naziyesa ndalama zopereka m’nyumba ya Yehova.
11 Napereka ndalama zoyesedwa m’manja mwa iwo akuchita ntchitoyi, akuyang’anira nyumba ya Yehova; ndipo iwo analipira nazo amisiri a mitengo ndi omanga, akugwira ntchito ya pa nyumba ya Yehova,
12 ndi omanga miyala ndi osema miyala, ndi kugula mitengo ndi miyala yosema kukakonza mogamuka nyumba ya Yehova, ndi zonse zoigulira nyumba zoikonzera.
13 Koma sanapangire nyumba ya Yehova mbale zasiliva, mbano, mbale zowazira, malipenga, zotengera zilizonse zagolide, kapena zotengera zilizonse zasiliva, kuzipanga ndi ndalama adabwera nazo kunyumba ya Yehova;
14 pakuti anazipereka kwa iwo akugwira ntchitoyi, nakonza nazo nyumba ya Yehova.
15 Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m’manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.
16 Ndalama za nsembe zopalamula ndi ndalama za nsembe yauchimo sanabwere nazo kunyumba ya Yehova; nza ansembe izi.
Yowasi agonja kwa Hazaele mfumu ya Aramu
17 Pamenepo Hazaele mfumu ya Aramu anakwera, nathira nkhondo pa Gati, naulanda, nalunjikitsa nkhope yake kukwera ku Yerusalemu.
18 Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zopatulika zonse adazipatula Yehosafati, ndi Yehoramu, ndi Ahaziya, makolo ake, mafumu a Yuda, ndi zopatulika zakezake, ndi golide yense anampeza pa chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Hazaele mfumu ya Aramu; motero anabwerera kuchoka ku Yerusalemu.
19 Machitidwe ena tsono a Yowasi ndi zonse adazichita sizinalembedwe kodi m’buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
20 Ndipo anyamata ake ananyamuka, napangana, nakantha Yowasi kunyumba ya Milo potsikira ku Sila.
21 Pakuti Yozakara mwana wa Simeati, ndi Yehozabadi mwana wa Somere, anyamata ake, anamkantha, nafa iye; ndipo anamuika kwa makolo ake m’mzinda wa Davide; ndi Amaziya mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/12-13d6fb3e643593576c6027b830fdf6f2.mp3?version_id=1068—