Yosiya wabwino akonzanso Kachisi
1 Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu chimodzi muYerusalemu; ndi dzina la make ndi Yedida mwana wa Adaya wa ku Bozikati.
2 Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, nayenda m’njira yonse ya Davide kholo lake, osapatukira ku dzanja lamanja kapena kulamanzere.
3 Ndipo kunali chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yosiya, mfumuyi inatuma Safani mwana wa Azaliya mwana wa Mesulamu, mlembi, kunyumba ya Yehova, ndi kuti,
4 Kwera kwa Hilikiya mkulu wa ansembe, awerenge ndalama zimene anthu anabwera nazo kunyumba ya Yehova,
5 ndizo zimene olindira pakhomo anasonkhetsa anthu; azipereke m’dzanja la antchito akuyang’anira nyumba ya Yehova; iwo azipereke kwa ogwira ntchito ya m’nyumba ya Yehova, akonze mogamuka nyumbayi,
6 kwa amisiri a mitengo, ndi omanga nyumba, ndi omanga linga; ndi kuti agule mitengo ndi miyala yosema kukonza nazo nyumbayi.
7 Koma sanawawerengere ndalamazo zoperekedwa m’dzanja lao, pakuti anachita mokhulupirika.
Hilikiya apeza buku la chilamulo
8 Ndipo Hilikiya mkulu wa ansembe anati kwa Safani mlembi, Ndapeza buku la chilamulo m’nyumba ya Yehova. Napereka Hilikiya bukulo kwa Safani, iye naliwerenga.
9 Ndipo Safani mlembiyo anadza kwa mfumu, nambwezera mfumu mau, nati, Anyamata anu anakhuthula ndalama zopereka m’nyumba, nazipereka m’dzanja la antchito akuyang’anira nyumba ya Yehova.
10 Ndipo Safani mlembiyo anafotokozera mfumu, ndi kuti, Hilikiya wansembe wandipatsa buku. Nawerengamo Safani pamaso pa mfumu.
11 Ndipo kunali, atamva mfumu mau a m’buku la chilamulo, inang’amba zovala zake.
12 Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu mwana wa Safani, ndi Akibori mwana wa Mikaya, ndi Safani mlembi, ndi Asaya mnyamata wa mfumu, ndi kuti,
13 Mukani, funsirani ine, ndi anthu, ndi Yuda yense, kwa Yehova za mau a buku ili adalipeza; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvere mau a buku ili, kuchita monga mwa zonse zotilemberamo.
Hulida mneneri wamkazi
14 Namuka Hilikiya wansembe, ndi Ahikamu, ndi Akibori, ndi Safani, ndi Asaya, kwa Hulidamneneriwamkazi, ndiye mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala za mfumu; analikukhala iye mu Yerusalemu m’dera lachiwiri, nalankhula naye.
15 Ndipo Hulida ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Muuze munthuyo anakutumizani kwa ine,
16 Atero Yehova, Taonani, nditengera malo ano choipa, ndi iwo okhalamo, chokwaniritsa mau onse a m’buku adaliwerenga mfumu ya Yuda;
17 popeza anandisiya Ine, nafukizira zonunkhira milungu ina, kuti autse mkwiyo wanga ndi ntchito zonse za manja ao; chifukwa chake mkwiyo wanga udzayakira malo ano wosazimikanso.
18 Koma kwa mfumu ya Yuda amene anakutumizani kufunsira kwa Yehova, muzitero naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Kunena za mau udawamva,
19 popeza mtima wako ngoolowa, ndipo unadzichepetsa pamaso pa Yehova muja udamva zonenera Ine malo ano ndi anthu okhalamo, kuti adzakhala abwinja, ndi temberero; ndipo unang’amba zovala zako ndi kulira misozi pamaso panga, Inenso ndakumvera, ati Yehova.
20 Chifukwa chake, taona, ndidzakusonkhanitsa ukhale ndi makolo ako, nudzatengedwa ulowe m’manda mwako mumtendere; ndipo sudzaona m’maso mwako choipa chonse ndidzachifikitsira malo ano. Ndipo anambwezera mfumu mau.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2KI/22-120fa1f6395fe1286d98d295727db481.mp3?version_id=1068—