Categories
1 MBIRI

1 MBIRI 10

Za imfa ya Saulo ndi ana ake

1 Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israele; ndipo amuna a Israele anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa paphiri la Gilibowa.

2 Ndipo Afilisti anaumirira kutsata Saulo ndi ana ake, ndi Afilistiwo anapha Yonatani, ndi Abinadabu, ndi Malikisuwa, ana a Saulo.

3 Ndi nkhondoyi inamkulira Saulo, ndi amauta anampeza; ndipo anatenga nkhawa chifukwa cha amauta.

4 Pamenepo Saulo anati kwa wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, nundipyoze nalo, angafike osadulidwa awa ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana, popeza anaopa kwambiri. Pomwepo Saulo anatenga lupanga lake, naligwera.

5 Ndipo pamene wonyamula zida zake anaona kuti Saulo wafa, anagwera nayenso lupanga lake, nafa.

6 Momwemo anafa Saulo, ndi ana ake atatu; ndi nyumba yake yonse idafa pamodzi.

7 Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m’chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya mizinda yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m’menemo.

8 Ndipo m’mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa paphiri la Gilibowa.

9 Ndipo anamvula natenga mutu wake, ndi zida zake, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m’mafano ao ndi mwa anthu.

10 Ndipo anaika zida zake m’nyumba ya milungu yao, napachika mutu wake m’nyumba ya Dagoni.

11 Ndipo onse a Yabesi-Giliyadi, atamva zonse Afilisti adachitira Saulo,

12 anauka ngwazi zonse, nachotsa mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, nabwera nayo ku Yabesi, naika mafupa ao patsinde pa mtengo wathundu ku Yabesi, nasala masiku asanu ndi awiri.

13 Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,

14 osafunsira kwa Yehova; chifukwa chake anamupha, napambutsira ufumu kwa Davide mwana wa Yese.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/10-ce37474650a18e5fe6c6cf04d4c913c0.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *