Davide awerenga anthu, mliri ugwera Israele
1 PamenepoSatanaanaukira Israele, nasonkhezera Davide awerenge Israele.
2 Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi kwa akulu a anthu, Kawerengeni Israele kuyambira ku Beereseba kufikira ku Dani; nimundibwezere mau, kuti ndidziwe chiwerengo chao.
3 Nati Yowabu, Yehova aonjezere pa anthu ake monga ali kazana; koma, mbuyanga mfumu, sali onse anyamata akapolo a mbuyanga? Nanga afuniranji chinthuchi mbuyanga, adzapalamulitsa Israele bwanji?
4 Koma mau a mfumu anamtsutsa Yowabu. Natuluka Yowabu, nakayendayenda mwa Aisraele onse, nadza kuYerusalemu.
5 Ndipo Yowabu anapereka kwa Davide chiwerengo cha anthu owerengedwa. Ndipo Aisraele onse anali zikwi mazana khumi ndi limodzi osolola lupanga, ndi Yuda anali zikwi mazana anai mphambu makumi asanu ndi awiri akusolola lupanga.
6 Koma sanawerenge Alevi ndi Abenjamini pakati pao; pakuti mau a mfumu anamnyansira Yowabu.
7 Ndipo Mulungu anaipidwa nacho chinthuchi, chifukwa chake Iye anakantha Israele.
8 Pamenepo Davide anati kwa Mulungu, Ndachimwa kwakukulu ndi kuchita chinthu ichi; koma tsopano, muchotse mphulupulu ya kapolo wanu, pakuti ndachita kopusa ndithu.
9 Ndipo Yehova ananena ndi Gadi mlauli wa Davide, ndi kuti,
10 Kanene kwa Davide kuti, Atero Yehova, Ndikuikira zitatu; dzisankhireko chimodzi ndikuchitire ichi.
11 Nadza Gadi kwa Davide, nanena naye, Atero Yehova, Dzitengereko;
12 kapena zaka zitatu za njala; kapena miyezi itatu ya kuthedwa pamaso pa adani ako, ndi kuti lupanga la adani ako likupeze; kapena masiku atatu lupanga la Yehova, ndilo mliri m’dzikomo, ndi mthenga wakuononga wa Yehova mwa malire onse a Israele. Ulingirire tsono, ndimbwezere mau anji Iye amene anandituma ine?
13 Ndipo Davide anati kwa Gadi, Ndipsinjika kwambiri; ndigwere m’dzanja la Yehova, pakuti zifundo zake zichulukadi; koma ndisagwere m’dzanja la munthu.
14 Momwemo Yehova anatumiza mliri pa Israele; ndipo adagwapo amuna zikwi makumi asanu ndi awiri a Israele.
Davide amangira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani
15 Ndipo Mulungu anatuma mthenga ku Yerusalemu kuuononga; ndipo poti auononge, Yehova anapenya, naleka choipachi; nati kwa mthenga wakuononga, Chakwanira, bweza dzanja lako tsopano. Ndi mthenga wa Yehova anaima pa dwale la Orinani Myebusi.
16 Ndipo Davide anakweza maso ake, naona mthenga wa Yehova alikuima pakati padziko ndi thambo, ali nalo lupanga losolola m’dzanja lake, lotambasukira pa Yerusalemu. Pamenepo Davide ndi akulu ovala ziguduli anagwa nkhope zao pansi.
17 Ndipo Davide anati kwa Mulungu, Si ndine nanga ndalamulira kuti awerenge anthu? Inde, ndine amene ndachimwa ndi kuchita choipa ndithu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu, Yehova Mulungu wanga, linditsutse ine ndi nyumba ya atate wanga, koma lisatsutse anthu anu ndi kuwachitira mliri.
18 Pamenepo mthenga wa Yehova analamula Gadi kuti anene ndi Davide, akwere Davideyo kuutsira Yehova guwa la nsembe pa dwale la Orinani Myebusi.
19 Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m’dzina la Yehova.
20 Pocheuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ake aamuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu.
21 Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, natuluka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yake pansi.
22 Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse ili pa mtengo wake wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.
23 Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu ichite chomkomera m’maso mwake; taonani, ndikupatsani ng’ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.
24 Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, Iai, koma ndidzaligula pa mtengo wake wonse; pakuti sindidzatengera Yehova chili chako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wake.
25 Momwemo Davide anapatsa Orinani chogulira malowa golide wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwake.
26 Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m’mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.
27 Ndipo Yehova analamula wamthenga kuti abweze lupanga lake m’chimake.
28 Nthawi yomweyi, pakuona Davide kuti Yehova anamvomereza pa dwale la Orinani Myebusi, anaphera nsembe pomwepo.
29 Pakuti chihema cha Yehova amene Mose anapanga m’chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi.
30 Koma Davide sanathe kumuka kukhomo kwake kufunsira kwa Mulungu, pakuti anaopa lupanga la mthenga wa Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/1CH/21-f0149d4cadfbfa1c2401749a06460bed.mp3?version_id=1068—