Asa apangana ndi Benihadadi, nalimbana ndi Israele
1 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.
2 Pamenepo Asa anatulutsasilivandi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,
3 Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golide; mukani, pasulani pangano lanu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.
4 Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi mizinda ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi mizinda yonse ya chuma ya Nafutali.
5 Ndipo kunali, pakumva ichi Baasa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa ntchito yake.
6 Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yake, imene Baasa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.
Hanani mlauli adzudzula Asa
7 Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m’dzanja lanu.
8 Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m’dzanja mwanu?
9 Pakuti maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m’menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.
10 Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m’kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.
11 Ndipo taonani, zochita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele.
12 Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafune Yehova, koma asing’anga.
13 Nagona Asa ndi makolo ake, namwalira atakhala mfumu zaka makumi anai.
14 Ndipo anamuika m’manda ake adadzisemerawo m’mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/16-f8b7e7e6c2d74b44ff18accd71bbe43a.mp3?version_id=1068—