Ukoma ndi ukulu wa Yehosafati
1 Ndipo Yehosafati mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake, nadzilimbitsa kuyambana ndi Israele.
2 Naika ankhondo m’mizinda yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m’dziko la Yuda, ndi m’mizinda ya Efuremu, imene adailanda Asa atate wake.
3 Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m’njira zake zoyamba za kholo lake Davide, osafuna Abaala;
4 koma anafuna Mulungu wa kholo lake nayenda m’malamulo ake, osatsata machitidwe a Israele.
5 Chifukwa chake Yehova anakhazikitsa ufumuwo m’dzanja lake, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamchulukira chuma ndi ulemu.
6 Ndi mtima wake unakwezeka m’njira za Yehova; anachotsanso misanje ndi zifanizo mu Yuda.
7 Chaka chachitatu cha ufumu wake anatuma akalonga ake, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netanele, ndi Mikaya, aphunzitse m’mizinda ya Yuda;
8 ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asahele, ndi Semiramoti, ndi Yehonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yehoramu, ansembe.
9 Ndipo anaphunzitsa mu Yuda ali nalo buku la chilamulo la Yehova, nayendayenda m’mizinda yonse ya Yuda, naphunzitsa mwa anthu.
10 Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambane ndi Yehosafati.
11 Ndipo Afilisti ena anabwera nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.
12 Ndipo Yehosafati anakula chikulire, namanga mu Yuda nyumba zansanja, ndi mizinda ya chuma.
13 Nakhala nazo ntchito zambiri m’mizinda ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu muYerusalemu.
14 Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akulu a zikwi; Adina wamkulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;
15 ndi wotsatana naye mkulu Yehohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;
16 ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikiri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri;
17 ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;
18 wotsatana naye Yehozabadi, ndi pamodzi ndi iye okonzekeratu kunkhondo zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu.
19 Ndiwo amene analindirira mfumu, osawerenga iwo aja mfumu adawaika m’mizinda yamalinga mu Yuda monse.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/17-fbc2893605d2a4d8c5683c10e6df1395.mp3?version_id=1068—