Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 23

Yehoyada adzoza Yowasi akhale mfumu

1 Koma chaka chachisanu ndi chiwiri Yehoyada anadzilimbitsa natenga atsogoleri a mazana, Azariya mwana wa Yerohamu, ndi Ismaele mwana wa Yehohanani, ndi Azariya mwana wa Obedi, ndi Maaseiya mwana wa Adaya, ndi Elisafati mwana wa Zikiri, apangane naye pamodzi.

2 Ndipo iwo anayendayenda mwa Yuda, nasonkhanitsa Alevi m’mizinda yonse ya Yuda, ndi akulu a nyumba za makolo mu Israele; nadza iwo kuYerusalemu.

3 Ndipo msonkhano wonse unapangana pangano ndi mfumu m’nyumba ya Mulungu. Ndipo ananena nao, Taonani, mwana wa mfumu adzakhala mfumu monga Yehova ananena za ana a Davide.

4 Chimene muzichita ndi ichi: limodzi la magawo atatu mwa inu olowera tsiku laSabata, la ansembe ndi Alevi, akhale olindirira pakhomo;

5 ndi limodzi la magawo atatu likhale kunyumba ya mfumu; ndi limodzi la magawo atatu ku Chipata cha Maziko; ndi anthu onse akhale m’mabwalo a nyumba ya Yehova.

6 Koma asalowe mmodzi m’nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.

7 Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zake m’dzanja mwake; ndipo aliyense wolowa m’nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakutuluka iye.

8 Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anachita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ake alowe tsiku la Sabata pamodzi ndi otuluka tsiku la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasule zigawo.

9 Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi malaya achitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m’nyumba ya Mulungu.

10 Ndipo anaika anthu onse, yense ndi chida chake m’dzanja lake, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya kudzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya kudzanja lamanzere la nyumba, kuloza kuguwa la nsembe ndi kunyumba.

11 Pamenepo anatulutsa mwana wa mfumu, namveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ake anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.

Aphedwa Ataliya

12 Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m’nyumba ya Yehova;

13 napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yake polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m’dziko anakondwera, naomba amalipenga; oimbira omwe analiko ndi zoimbirazo, nalangiza poimbira cholemekeza. Pamenepo Ataliya anang’amba zovala zake, nati, Chiwembu, chiwembu.

14 Koma Yehoyada wansembe anatuluka nao atsogoleri a mazana akuyang’anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mtulutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo aliyense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m’nyumba ya Yehova.

15 Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku Chipata cha Akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.

Pangano la Yehoyada wansembe

16 Ndipo Yehoyada anachita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.

17 Ndi anthu onse anamuka kunyumba yaBaala, naipasula, naphwanya maguwa ake a nsembe, ndi mafano ake; namupha Matani wansembe wa Baala kumaguwa a nsembe.

18 Ndipo Yehoyada anaika mayang’aniro a nyumba ya Yehova m’dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang’anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m’chilamulo cha Mose, ndi kukondwera ndi kuimbira, monga mwa chilangizo cha Davide.

19 Ndipo anaika odikira kumakomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kalikonse asalowemo.

20 Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m’dziko, natsika ndi mfumu kunyumba ya Yehova; nalowera pa chipata cha kumtunda m’nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.

21 Ndipo anthu onse a m’dziko anakondwera; ndi m’mzinda munali chete, atamupha Ataliya ndi lupanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/23-0620229be82c1bca9e3ee495dce24e59.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *