Hezekiya achita Paska ku Yerusalemu
1 Ndipo Hezekiya anatumiza kwa Israele ndi Yuda onse, nalembanso makalata kwa Efuremu ndi Manase, kuti abwere kunyumba ya Yehova kuYerusalemu, kuchitira Yehova Mulungu wa IsraelePaska.
2 Pakuti mfumu idapangana ndi akulu ake, ndi msonkhano wonse wa mu Yerusalemu, kuti achite Paska mwezi wachiwiri.
3 Pakuti sanakhoze kumchita nthawi ija, popeza ansembe odzipatulira sanafikire, ndi anthu sadasonkhane ku Yerusalemu.
4 Ndipo chinthuchi chinayenera m’maso mwa mfumu ndi msonkhano wonse.
5 Motero anakhazikitsa mau kulalikira mwa Israele lonse, kuyambira Beereseba kufikira ku Dani, kuti abwere kuchitira Yehova Mulungu wa Israele Paska ku Yerusalemu; pakuti nthawi yaikulu sanachite monga mudalembedwa.
6 Tsono amtokoma anamuka ndi makalata ofuma kwa mfumu ndi akulu ake mwa Israele ndi Yuda lonse, monga inauza mfumu ndi kuti, Inu ana a Israele, bwerani kwa Yehova Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Israele, kuti Iye abwere kwa otsala anu opulumuka m’dzanja la mafumu a Asiriya.
7 Ndipo musamakhala ngati makolo anu ndi abale anu, amene analakwira Yehova Mulungu wa makolo ao, motero kuti anawapereka apasuke, monga mupenya.
8 Musamakhala ouma khosi monga makolo anu; koma gwiranani dzanja ndi Yehova, nimulowe m’malo ake opatulika, amene anapatula kosatha, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu; kuti mkwiyo wake waukali utembenuke kwa inu.
9 Pakuti mukabwera kwa Yehova, abale anu ndi ana anu adzapeza chifundo pamaso pa iwo anawatenga ndende, nadzalowanso m’dziko muno; pakuti Yehova Mulungu wanu ngwa chisomo ndi chifundo; sadzakuyang’anirani kumbali ngati mubwera kwa Iye.
10 Ndipo amtokoma anapitira m’mizinda yonse ya dziko la Efuremu ndi Manase, mpaka Zebuloni; koma anawaseka pwepwete nawanyodola.
11 Komatu ena a Asere ndi Manase ndi a Zebuloni anadzichepetsa, nadza ku Yerusalemu.
12 Ku Yuda komwe kunali dzanja la Mulungu lakuwapatsa mtima umodzi, kuchita chowauza mfumu ndi akulu mwa mau a Yehova.
13 Nasonkhana ku Yerusalemu anthu ambiri kuchitachikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsamwezi wachiwiri, msonkhano waukulu ndithu.
14 Ndipo anauka nachotsa maguwa a nsembe okhala mu Yerusalemu, nachotsa pofukizira zonunkhira, naziponya m’mtsinje wa Kidroni.
15 Pamenepo anaphera Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi wachiwiri, ndipo ansembe ndi Alevi anachita manyazi, nadzipatula, nabwera nazo nsembe zopsereza kunyumba ya Yehova.
16 Naima m’malo mwao mwa kulongosoka kwao, monga mwa chilamulo cha Mose munthu wa Mulunguyo; ansembe anawaza mwazi, ataulandira kudzanja la Alevi.
17 Pakuti munali ambiri mumsonkhano sanadzipatule; potero Alevi anayang’anira kupha za Paska kwa aliyense wosakhala woyera, kuwapatulira Yehova.
18 Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efuremu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretse, koma anadya Paska mosati monga munalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense
19 wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.
20 Ndipo Yehova anamvera Hezekiya, nawachiritsa anthu.
21 Ndipo ana a Israele opezeka mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe chachikulu; ndi Alevi ndi ansembe analemekeza Yehova tsiku ndi tsiku ndi zoimbira zakuliritsa kwa Yehova.
22 Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.
23 Ndipo msonkhano wonse unapangana kuchita masiku asanu ndi awiri ena, nachita masiku asanu ndi ena ndi chimwemwe.
24 Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng’ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akulu anapatsa msonkhano ng’ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembe ambiri adadzipatula.
25 Ndi msonkhano wonse wa Yuda, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi, ndi msonkhano wonse wochokera kwa Israele, ndi alendo ochokera kudziko la Israele, ndi okhala mu Yuda, anakondwera.
26 Momwemo munali chimwemwe chachikulu mu Yerusalemu; pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israele simunachitike chotero mu Yerusalemu.
27 Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/30-7956a3ac55adff94fc09babbf82998de.mp3?version_id=1068—