Categories
2 MBIRI

2 MBIRI 32

Senakeribu agwera Yuda

1 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Senakeribu mfumu ya Asiriya, nalowera Yuda, namangira mizinda yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.

2 Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Senakeribu, ndi kuti nkhope yake inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndiYerusalemu,

3 anapangana ndi akulu ake ndi amphamvu ake, kutseka madzi a mu akasupe okhala kunja kwa mzinda; namthandiza iwo.

4 Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati padziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asiriya ndi kupeza madzi ambiri.

5 Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwake, nalimbitsa Milo m’mzinda wa Davide, napanga zida ndi zikopa zochuluka.

6 Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye kubwalo la kuchipata cha mzinda, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti,

7 Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena kutenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asiriya ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe achuluka koposa okhala naye;

8 pamodzi ndi iye pali dzanja la thupi lanyama; koma pamodzi ndi ife pali Yehova Mulungu wathu, kutithandiza ndi kutigwirira nkhondo. Ndipo anthu anachirikizika ndi mau a Hezekiya mfumu ya Yuda.

9 Pambuyo pake Senakeribu mfumu ya Asiriya, akali ku Lakisi ndi mphamvu yake yonse pamodzi naye, anatuma anyamata kwa Hezekiya mfumu ya Yuda, ndi kwa Ayuda onse okhala ku Yerusalemu, ndi kuti,

10 Atero Senakeribu mfumu ya Asiriya, Mutama chiyani kuti mukhala m’linga mu Yerusalemu?

11 Sakukopani Hezekiya, kuti akuperekeni mufe nayo njala ndi ludzu, ndi kuti, Yehova Mulungu wathu adzatilanditsa m’dzanja la mfumu ya Asiriya?

12 Sanaichotse misanje yake ndi maguwa ake a nsembe Hezekiya yemweyo, nauza Yuda ndi Yerusalemu, ndi kuti, Mugwadire kuguwa la nsembe limodzi ndi kufukiza zonunkhira pamenepo?

13 Simudziwa kodi chomwe ine ndi makolo anga tachitira anthu onse a m’maikomo? Kodi milungu ya mitundu ya anthu inakhoza konse kulanditsa dziko lao m’dzanja langa?

14 Ndi uti mwa milungu yonse ya mitunduyi ya anthu, amene makolo anga anawaononga konse, unakhoza kulanditsa anthu ake m’dzanja mwanga?

15 Ndipo tsono, asakunyengeni Hezekiya, ndi kukukopani motero, musamkhulupirira; pakuti palibe Mulungu wa mtundu uliwonse wa anthu, kapena ufumu uliwonse, unakhoza kulanditsa anthu ake m’dzanja mwanga; ndipo kodi Mulungu wanu adzakulanditsani inu m’dzanja langa?

16 Ndipo anyamata ake anaonjeza kunena motsutsana ndi Yehova Mulungu, ndi mnyamata wake Hezekiya.

17 Analemberanso makalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m’maiko, imene siinalanditse anthu ao m’dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m’dzanja mwanga.

18 Ndipo anafuula ndi mau aakulu m’chinenedwe cha Ayuda kwa anthu a mu Yerusalemu okhala palinga, kuwaopsa ndi kuwavuta, kuti alande mzindawu.

19 Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a padziko lapansi, ndiyo ntchito ya manja a anthu.

20 Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesayamnenerimwana wa Amozi, anapemphera pa ichi, nafuulira Kumwamba.

21 Ndipo Yehova anatuma wamthenga amene anaononga ngwazi zamphamvu zonse, ndi atsogoleri, ndi akazembe, kuchigono cha mfumu ya Asiriya. Nabwerera iye ndi nkhope yamanyazi kudziko lake. Ndipo atalowa m’nyumba ya mulungu wake, iwo otuluka m’matumbo mwake anamupha ndi lupanga pomwepo.

22 Momwemo Yehova analanditsa Hezekiya ndi okhala mu Yerusalemu m’dzanja la Senakeribu mfumu ya Asiriya, ndi m’dzanja la onse ena, nawatsogolera monsemo.

23 Ndipo ambiri anabwera nayo mitulo kwa Yehova ku Yerusalemu, ndi za mtengo wake, kwa Hezekiya mfumu ya Yuda; nakwezeka iye pamaso paamitunduonse kuyambira pomwepo.

Nthenda ndi imfa ya Hezekiya

24 Masiku omwe aja Hezekiya anadwala pafupi imfa; ndipo anapemphera kwa Yehova; ndi Iye ananena naye, nampatsa chizindikiro chodabwitsa.

25 Koma Hezekiya sanabwezere monga mwa chokoma anamchitira, pakuti mtima wake unakwezeka; chifukwa chake unamdzera mkwiyo iye, ndi Yuda, ndi Yerusalemu.

26 Koma Hezekiya anadzichepetsa m’kudzikuza kwa mtima wake, iye ndi okhala mu Yerusalemu, momwemo mkwiyo wa Yehova sunawadzere masiku a Hezekiya.

27 Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramosiliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse;

28 ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iliyonse, ndi makola a zoweta.

29 Nadzimangiranso mizinda, nadzionera nkhosa ndi ng’ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri.

30 Hezekiya yemweyo anatseka kasupe wa kumtunda wa madzi a Gihoni, nawapambutsa atsikire kumadzulo kwa mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya analemerera nazo ntchito zake zonse.

31 Koma pokhala naye akazembe a akalonga a ku Babiloni, amene anatumiza kwa iye kufunsira za chodabwitsa chija chidachitika m’dzikomo, Mulungu anamsiya, kumuyesa, kuti adziwe zonse za mumtima mwake.

32 Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi ntchito zake zokoma, taonani, zilembedwa m’masomphenya a Yesaya mneneri mwana wa Amozi, ndi m’buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

33 Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala mu Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m’malo mwake.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/2CH/32-992fffafd25659057ef3d5ff6461ed3d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *