Categories
EZARA

EZARA 4

Asamariya aneneza Ayuda omanga Kachisi kwa Ahasuwero

1 Atamva tsono adani a Yuda ndi Benjamini kuti ana aja a ndende analikumangira Yehova Mulungu wa Israele Kachisi,

2 anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno.

3 Koma Zerubabele, ndi Yesuwa, ndi akulu otsala a nyumba za makolo a Israele, anati kwa iwo, Sikuyenera ndi inu ndi ife kumangira Mulungu wathu nyumba, koma ife tokha pamodzi tidzamangira Yehova Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi mfumu ya Persiya watilamulira.

4 Pamenepo anthu a m’dziko anafoketsa manja a anthu Ayuda, nawavuta pomanga,

5 nalembera opangira atsutsane nao, nafafanize uphungu wao, masiku onse a Kirusi mfumu ya Persiya, mpaka ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.

6 Ndipo pokhala mfumu Ahasuwero, poyambira ufumu wake, analembera chowaneneza okhala mu Yuda ndi muYerusalemu.

7 Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba mu Chiaramu, namsanduliza mu Chiaramu.

8 Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, analemba kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi, wakutsutsana naye Yerusalemu motere:

9 nalembera Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi Simisai mlembi, ndi anzake otsala; Adinai, ndi Afarisatikai, Ataripilai, Afarisai, Aereke, Ababiloni, Asusani, Adehai, Aelamu,

10 ndiamitunduotsala amene, Osinapara wamkulu ndi womveka adawatenga mikoli, nawakhalitsa m’mizinda ya Samariya, ndi m’dziko lotsala tsidya lino la mtsinje wa Yufurate.

11 Zolembedwa m’kalatayo anazitumiza kwa Arita-kisereksesi mfumu: ife akapolo anu, anthu a tsidya lino la mtsinjewo, tikupatsani moni.

12 Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mzinda uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake.

13 Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mzinda uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m’njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu.

14 Popeza tsono timadya mchere wa m’nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; chifukwa chake tatumiza ndi kudziwitsa mfumu,

15 kuti afunefune m’buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m’buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mzinda uwu ndi mzinda wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m’menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mzinda uwu.

16 Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mzindawu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.

Mfumu iwaletsa asamange Kachisi

17 Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala mu Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Moni, ndi nthawi yakuti.

18 Kalatayo mwatitumizira anandiwerengera momveka.

19 Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mzinda uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe, ndi kuti akachitamo mpanduko ndi kudziyendera.

20 Panalinso mafumu amphamvu mu Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m’njira.

21 Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mzinda uwu, mpaka ndidzalamulira ndine.

22 Chenjerani mungadodomepo, chidzakuliranji chisauko cha kusowetsa mafumu?

23 Pamenepo atawerenga malemba a kalata ya mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.

24 Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/4-82a07869b218914d2883af4d0ac3377e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *