Categories
EZARA

EZARA 5

Zerubabele ndi Yesuwa apitirira kumanga Kachisi

1 Ndipo aneneri, Hagaimneneriyo, ndi Zekariya mwana wa Ido, ananenera kwa Ayuda okhala mu Yuda ndi muYerusalemu; m’dzina la Mulungu wa Israele ananenera kwa iwo.

2 Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.

3 Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

4 Nanena naonso motere, Maina ao a anthu omanga chimangidwe ichi ndiwo ayani?

5 Koma diso la Mulungu wao linali pa akulu a Ayuda, ndipo sanawaletse mpaka mlandu unamdzera Dariusi, nabweza mau a mlanduwo m’kalata.

Tatenai awaneneza kwa Dariusi

6 Zolembedwa m’kalata amene Tatenai kazembe wa tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzake Afarisikai, okhala tsidya lino la mtsinje, anatumiza kwa Dariusi mfumu,

7 anatumiza kalata kwa iyeyo m’menemo munalembedwa motere, kwa Dariusi mfumu, mtendere wonse.

8 Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, ndi kuikidwa mitengo pamakoma, ndipo inachitika mofulumira ntchitoyi, ndipo inayenda bwino m’dzanja mwao.

9 Pamenepo tinafunsa akulu aja ndi kutere nao, Anakulamulirani ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?

10 Tinawafunsanso maina ao, kukudziwitsani, kuti tilembere maina a anthu akuwatsogolera.

11 Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi, tilikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikulu ya Israele.

12 Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m’dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni Mkaldeya, amene anaononga nyumba ino, natenga anthu ndende kunka nao ku Babiloni.

13 Koma chaka choyamba cha Kirusi mfumu ya Babiloni, Kirusi mfumuyo analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu.

14 Ndiponso zipangizo za golide ndisilivaza nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara mu Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa mu Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;

15 nati naye, Tenga zipangizo izi, kaziike mu Kachisi ali mu Yerusalemu, nimangidwe nyumba ya Mulungu pambuto pake.

16 Pamenepo anadza Sezibazara yemweyo namanga maziko a nyumba ya Mulungu ili mu Yerusalemu; ndipo kuyambira pomwepo kufikira tsopano ilinkumangidwa, koma siinatsirizike.

17 Ndipo tsono chikakomera mfumu, munthu asanthule m’nyumba ya chuma cha mfumu ili komwe ku Babiloni, ngati nkuterodi, kuti Kirusi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa chinthuchi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/EZR/5-90c7b1f322227b04a56b144ddac47a5b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *