Arita-kisereksesi alola Nehemiya akamange linga la Yerusalemu
1 Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.
2 Ninena nane mfumu, Nkhope yako nja chisoni chifukwa ninji popeza sudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mtima. Pamenepo ndinachita mantha aakulu.
3 Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumzinda kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.
4 Ndipo mfumu inati kwa ine, Ufunanji iwe? Pamenepo ndinapemphera Mulungu wa Kumwamba.
5 Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumzinda wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.
6 Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi.
7 Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse makalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;
8 ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.
9 Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo.
10 Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.
11 Motero ndinafika kuYerusalemu, ndi kukhalako masiku atatu.
12 Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m’mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.
13 Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang’ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.
14 Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera.
15 Ndipo ndinakwera usiku kumtsinje, ndi kuyang’ana lingali; ndinabwerera tsono ndi kulowa pa Chipata cha ku Chigwa, momwemo ndinabwereranso.
16 Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi.
17 Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m’mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.
18 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.
19 Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?
20 Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam’mwamba, Iye ndiye adzatilemeretsa; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, mu Yerusalemu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/2-fcf0168cc29ad4b4756c1d382e516969.mp3?version_id=1068—