Adani ayesa kuwaletsa kumanga malinga
1 Ndipo kunali, atamva Sanibalati kuti tinalikumanga lingali, kudamuipira, nakwiya kwakukulu, naseka Ayuda pwepwete.
2 Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?
3 Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala.
4 Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere chitonzo chao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale chofunkhidwa m’dziko la ndende;
5 ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.
6 Koma tinamanga lingali, ndi linga lonse linalumikizana kufikira pakatimpakati; popeza mitima ya anthu inalunjika kuntchito.
7 Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga aYerusalemuanakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;
8 napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m’menemo.
9 Koma tinapemphera kwa Mulungu wathu, ndi kuwaikira olindirira usana ndi usiku, chifukwa cha iwowa.
10 Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.
11 Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.
12 Ndipo kunali, atafika Ayuda okhala pafupi pao ochokera pamalo ponse, anatiuza ife kakhumi, Bwererani kwa ife.
Ankhondo atchinjiriza antchito
13 Chifukwa chake ndinawaika potera m’kati mwa linga, popenyeka; inde ndinaika anthu monga mwa mabanja ao, akhale nao malupanga ao, nthungo zao, ndi mauta ao.
14 Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Ambuye wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu.
15 Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.
16 Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m’mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.
17 Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anachita aliyense ndi dzanja lake lina logwira ntchito, ndi lina logwira chida;
18 ndi omanga linga aliyense anamangirira lupanga lake m’chuuno mwake, nagwira ntchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine.
19 Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Ntchito ndiyo yochuluka ndi yachitando, ndi ife tili palakepalake palingapo, yense atalikizana ndi mnzake;
20 paliponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo.
21 Momwemo tinalikugwira ntchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbandakucha mpaka zatuluka nyenyezi.
22 Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone mu Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana.
23 Ndipo ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, angakhale amuna olindirira onditsata ine, nnena mmodzi yense wa ife anavula zovala zake, yense anapita ndi chida chake kumadzi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/4-38be6d4224d9a6addda239215b6fd0dd.mp3?version_id=1068—