Nehemiya atchinjiriza aumphawi opsinjika
1 Pamenepo panamveka kulira kwakukulu kwa anthu ndi akazi ao kudandaula pa abale ao Ayuda.
2 Popeza panali ena akuti, Ife, ana athu aamuna ndi aakazi, ndife ambiri; talandira tirigu, kuti tidye tikhale ndi moyo.
3 Panali enanso akuti, Tili kupereka chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa ndi nyumba zathu; kuti tilandire tirigu chifukwa cha njalayi.
4 Panali enanso akuti, Takongola ndalama za msonkho wa mfumu; taperekapo chikole minda yathu, ndi minda yathu yampesa.
5 Koma tsopano thupi lathu likunga thupi la abale athu, ana athu akunga ana ao; ndipo taonani, titengetsa ana athu aamuna ndi aakazi akhale akapolo, ndi ana athu aakazi ena tawatengetsa kale; ndipo tilibe ife mphamvu ya kuchitapo kanthu; ndi minda yathu, ndi minda yathu yampesa, nja ena.
6 Ndipo pakumva kulira kwao, ndi mau ao, kunandiipira kwambiri.
7 Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa.
8 Ndipo ndinanena nao, Ife monga umo tinakhoza, tinaombola abale athu Ayuda ogulitsidwa kwaamitundu; ndipo kodi inu mukuti mugulitse abale anu, kapena tiwagule ndi ife? Pamenepo anakhala duu, nasowa ponena.
9 Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m’kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?
10 Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.
11 Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao yaazitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.
12 Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa.
13 Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati,Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa.
14 Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m’dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadye chakudya cha kazembe.
15 Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndisilivamasekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.
16 Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligule, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.
17 Panalinso podyera ine Ayuda ndi olamulira amuna zana limodzi mphambu makumi asanu, pamodzi ndi iwo akutidzera kuchokera kwa amitundu otizinga.
18 Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng’ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsire chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.
19 Mundikumbukire Mulungu, zindikomere zonse ndinachitira anthu awa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/NEH/5-8f7b93e64342364ce1095bfb4cc368e7.mp3?version_id=1068—