Elifazi adzudzula Yobu
1 Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha, nati,
2 Munthu akayesa kunena nawe mau,
kodi udzamva nao chisoni?
Koma akhoza ndani kudziletsa kunena?
3 Taona iwe walangiza aunyinji,
walimbitsa manja a ofooka.
4 Mau ako anachirikiza iye amene akadagwa,
walimbitsanso maondo otewa.
5 Koma tsopano chakufikira iwe, ndipo ukomoka;
chikukhudza, ndipo uvutika.
6 Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu,
ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?
7 Takumbukira tsopano, watayika ndani wosapalamula konse?
Kapena oongoka mtima alikhidwa kuti?
8 Monga umo, ndaonera, olimira mphulupulu,
nabzala vuto, akololapo zomwezo.
9 Atayika ndi mpweya wa Mulungu,
nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.
10 Kubangula kwa mkango,
ndi kulira kwa mkango waukali kwaletsedwa,
ndi mano a misona ya mkango athyoledwa.
11 Mkango wokalamba udzifera posowa mkoka,
ndi misona ya mkango waukazi imwazika.
12 Anditengera mau m’tseri,
m’khutu mwanga ndinalandira kunong’oneza kwake.
13 M’malingaliro a masomphenya a usiku,
powagwira anthu tulo tatikulu
14 Anandidzera mantha ndi kunjenjemera,
nanthunthumira nako mafupa anga onse.
15 Pamenepo panapita mzimu pamaso panga;
tsitsi la thupi langa lidati nyaunyau.
16 Unaima chilili, koma sindinathe kuzindikira maonekedwe ake;
panali mzukwa pamaso panga;
kunali chete, ndipo ndidamva mau akuti,
17 Kodi munthu adzakhala wolungama ndi kuposa Mulungu?
Kodi munthu adzakhala woyera woposa Mlengi wake?
18 Taona, sakhulupirira atumiki ake;
nawanenera amithenga ake zopusa;
19 kopambana kotani nanga iwo akukhala m’nyumba zadothi,
amene kuzika kwao kuli m’fumbi,
angothudzulidwa ngati njenjete.
20 Kuyambira m’mawa kufikira madzulo athudzuka;
aonongeka kosatha, osasamalirako munthu.
21 Kukometsetsa kwao sikumachotsedwa nao?
Amafa koma opanda nzeru.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/4-c4008d5cfe7524034f6cf5fb55f3f00e.mp3?version_id=1068—