1 Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno?
Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?
2 Monga kapolo woliralira mthunzi,
monga wolembedwa ntchito ayembekezera mphotho yake,
3 momwemo anandilowetsa miyezi yopanda pake.
Nandiikiratu zowawa usiku ndi usiku.
4 Ndigona pansi, ndikuti,
Ndidzauka liti? Koma usiku undikulira;
ndipo ndimapalapata mpaka mbandakucha.
5 Mnofu wanga wavala mphutsi ndi nkanambo zadothi;
khungu langa lang’ambika, nilinyansa.
6 Masiku anga afulumira koposa mphindo ya muomba,
apitirira opanda chiyembekezo.
7 Kumbukira kuti moyo wanga ndiwo mphepo,
diso langa silidzaonanso chokoma.
8 Diso la amene andiona silidzandionanso,
maso ako adzandipenyetsetsa, koma ine palibe.
9 Mtambo wapita watha,
momwemo wakutsikira kumanda sadzakwerakonso.
10 Sadzabweranso kunyumba yake,
osamdziwanso malo ake.
11 Potero sindidzaletsa pakamwa panga;
ndidzalankhula popsinjika mu mzimu mwanga;
ndidzadandaula pakuwawa mtima wanga.
12 Ndine nyanja kodi, kapena chinjoka cha m’nyanja,
kuti Inu mundiikira odikira?
13 Ndikati, Pakama panga mpondisangalatsa,
pogona panga padzachepsa chondidandaulitsa;
14 pamenepo mundiopsa ndi maloto,
nimundichititsa mantha ndi masomphenya;
15 potero moyo wanga usankha kupotedwa,
ndi imfa, koposa mafupa anga awa.
16 Ndinyansidwa nao moyo wanga;
sindidzakhala ndi moyo chikhalire;
mundileke; pakuti masiku anga ndi achabe.
17 Munthu ndani kuti mumkuze,
ndi kuti muike mtima wanu pa iye,
18 ndi kuti mucheze naye m’mawa ndi m’mawa,
ndi kumuyesa nthawi zonse?
19 Mukana kundichokera kufikira liti,
kapena kundileka mpaka nditameza dovu?
20 Ngati ndachimwa, ndingachitire Inu chiyani,
Inu wodikira anthu?
Mwandiikiranji ndikhale chandamali chanu?
Kuti ndikhale kwa ine ndekha katundu?
21 Mulekeranji kukhululukira kulakwa kwanga
ndi kundichotsera mphulupulu yanga?
Popeza tsopano ndidzagona kufumbi;
mudzandifunafuna, koma ine palibe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/7-733b988db546a25ec801104bdc4ae2fc.mp3?version_id=1068—