1 Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika,
kumanda kwandikonzekeratu.
2 Zoonadi, ali nane ondiseka;
ndi diso langa lili chipenyere m’kundiwindula kwao.
3 Mupatse chigwiriro tsono,
mundikhalire chikole Inu nokha kwanu;
ndani adzapangana nane kundilipirira?
4 Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;
chifukwa chake simudzawakuza.
5 Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo,
m’maso mwa ana ake mudzada.
6 Anandiyesanso chitonzo cha anthu;
ndipo ndakhala ngati munthu womthira malovu pankhope pake.
7 M’diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni,
ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi.
8 Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho,
ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.
9 Koma wolungama asungitsa njira yake,
ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.
10 Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;
pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.
11 Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,
zakezake zomwe za mtima wanga.
12 Zisanduliza usiku ukhale usana;
kuunika kuyandikana ndi mdima.
13 Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;
ndikayala pogona panga mumdima.
14 Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;
kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;
15 chilikuti chiyembekezo changa?
Inde, chiyembekezo changa adzachiona ndani?
16 Chidzatsikira kumipingiridzo ya kumanda,
pamene tipumulira pamodzi kufumbi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/17-b338533e7f587ecaf82cea33fff5c062.mp3?version_id=1068—