Bilidadi atsutsa Yobu pa kudzikuza kwake, nanena za tsoka la oipa
1 Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha, nati,
2 Musaka mau kufikira liti?
Zindikirani, ndi pamenepo tidzanena.
3 Tiyesedwa bwanji ngati nyama zakuthengo,
ndi kukhala odetsedwa pamaso panu?
4 Iwe wodzing’amba mumkwiyo mwako,
kodi dziko lapansi lisiyidwe chifukwa cha iwe?
Kapena thanthwe lisunthike m’malo mwake?
5 Inde, kuunika kwa woipa kudzazima,
ndi lawi la moto wake silidzawala.
6 Kuunikaku kudzada m’hema mwake,
ndi nyali yake ya pamwamba pake idzazima.
7 Mapondedwe ake amphamvu adzasautsidwa,
ndi uphungu wakewake udzamgwetsa.
8 Pakuti aponyedwa mu ukonde ndi mapazi ake,
namaponda pamatanda.
9 Msampha udzamgwira kuchitendeni,
ndi khwekhwe lidzamkola.
10 Msampha woponda umbisikira pansi,
ndi msampha wa chipeto panjira.
11 Zoopetsa zidzamchititsa mantha monsemo,
nadzampirikitsa kumbuyo kwake.
12 Njala idzatha mphamvu yake,
ndi tsoka lidzamkonzekeratu pambali pake.
13 Zidzatha ziwalo za thupi lake,
mwana woyamba wa imfa adzatha ziwalo zake.
14 Adzazulidwa kuhema kwake kumene anakhulupirira;
nadzatengedwa kunka naye kwa mfumu ya zoopsa.
15 Adzakhala m’hema mwake iwo amene sali ake;
miyala yasulufureidzawazika pokhala pake.
16 Mizu yake idzauma pansi,
ndi nthambi yake idzafota m’mwamba.
17 Chikumbukiro chake chidzatayika m’dziko,
ndipo adzasowa dzina kukhwalala.
18 Adzamkankha achoke kukuunika alowe kumdima;
adzampirikitsa achoke m’dziko lokhalamo anthu.
19 Sadzakhala naye mwana kapena chidzukulu
mwa anthu a mtundu wake,
kapena wina wotsalira kumene anakhalako.
20 Akudza m’mbuyo adzadabwa nalo tsiku lake,
monga aja omtsogolera anagwidwa mantha.
21 Zoonadi, zokhalamo osalungama zitero,
ndi malo a iye amene sadziwa Mulungu ndi awa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/JOB/18-2872a6bcfc7f6d87ff987c4c91ec1b4e.mp3?version_id=1068—